Mkulu wa DODMA, wapampando wa komiti ya Covid-19 athotholedwa

Advertisement

Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera achotsa paudindo mkulu wa nthambi yowona za ngozi zogwa mwadzidzi komanso wapampando wa komiti yamtsogoleri wadziko pantchito yothana ndi mlili wa Covid-19 kaamba kakusakazidwa kwa ndalama za Covid-19.

A Chakwera anena izi lamulungu pa 14 February pomwe amayankhula ku mtundu wa a Malawi momwe dziko lino likuchitira pantchito yothana ndi mlili wa Covid-19.

Iwo ati mkulu wa nthambi yowona za ngozi zogwa mwadzidzi ya DODMA a James Chiusiwa komaso wapampando wa komiti yamtsogoleri wadziko pantchito yothana ndi Covid-19 Dr John Phuka, onse alephera pantchito zawo.

Iwo anati izi zikutsatila kafukufuku wa yemwe mkulu omva za madandaulo a anthu pazinthu zosiyanasiyana a Martha Chizuma anapanga chaka chatha yemwe anasonyeza kuti ndalama zankhaninkhani za Covid-19 zinasakazidwa.

Kafukufuku wa a Chizuma anaonetsa kuti ndalama zomwe zinapelekedwa ku nthambi ya DODMA zinagwiritsidwa ntchito kwambiri ngati ma alawasi kwa akuluakulu anthambiyi komaso makosana ena a komiti yamtsogoleri wadziko yothana ndi Covid-19.

A Chakwera ati pamwamba pazonsezi, akuluakulu othotholedwawa analephera kuonetsetsa kuti ndalama zomwe anapatsidwa zagwira ntchito yake bwino ndipo awopsezaso onse omwe akukhudzidwa ndikusokonekera kwa ndalamazi kuti amangidwa.

“Aliyense amene apezeke kuti anagwiritsa ntchito molokwika kapena anaba ndalama za Covid-19 Ku DODMA ngakhaleso kumakhonsolo, amangidwa,” atelo a Chakwera.

Mtsogoleri wadziko linoyu walamulaso kuti akuluakulu onse a makomiti ang’onoang’ono pa ntchito yothana ndi Covid-19 achotsedwe ntchito kaamba kolephera kupereka mndandanda wa momwe agwiritsira ntchito ndalama za Covid-19 zokwana K17 billion.

Pakadali pano a Chakwera asankha Dr Chalamila Nkhoma kulowa mmalo mwa Dr John Phuka ngati wapampando wa komiti ya mtsogoleri wadziko yothana ndi COVID-19 ndipo ati posachedwapa alengezaso yemwe alowe mmalo mwa a Chiusiwa ngati mkulu wa DODMA.

Mtsogoleri wa dziko linoyu walamuraso kuti bungwe la lothana ndi katangale la ACB komaso bungwe lomenyera ufulu wa anthu la MHRC awayika mu komiti yamtsogoleri wadziko yolimbikitsa kuthana ndi COVID-19.

Pakadali pano chipani chotsutsa boma cha DPP kudzera kwa mkulu oyang’ana nkhani zokhudza malamulo mchipanichi a Bright Msaka, chati ichi sichiganizo chabwino ponena kuti zipangitsa kuti mabungwe awiriwa asagwire ntchito yake bwino.

Advertisement