O’Laza awa ndi panja penipeni – katswiri wa za malamulo

Inu mukuti ulendo uwu ndi wa ku Kenani, kambani ina chifukwa o’Chakwera alibe olo dontho la utsogoleri mwa iwo, ndendende zinachoka zija.

Katswiri wa za malamulo, a Professor Danwood Chirwa athila ukali a Lazarus Chakwera kamba ka kulephela pa utsogoleri pa nkhani ya coronavirus ndinso kusowa kwa 6.2 biliyoni Kwacha.

Polemba pa tsamba lawo la mchezo la Facebook, a Chirwa amene amaphunzitsa pa sukulu ya ukachenjede ya Cape Town mu dziko la South Africa ati a Chakwera akudziwapo kanthu ndithu pa kusowa kwa 6.2 biliyoni yolimbanilana ndi matenda a Covid.

“Kutsata mmene ndalama izi zayendela kukungoonetsa chinyengo. A Pulezidenti akudziwa ndithu kapena akuyenela kudziwa kuti ma lipoti a momwe ndalama zayendela ndi chiphimba mmaso chabe. Izi achitila dala,” atelo a Chirwa.

Iwo adzudzulanso a Chakwera kamba kosaikapo mtima polimbana ndi matenda a Covid.

“Asanalowe m’boma, a Chakwera anapeputsa matendawa ndipo atalowa m’boma sikuti anasintha ayi. Mkuluyu anali pa kalikiliki kuyendayenda ndinso osaonetsa chidwi pa zipatala,” atelo a Chirwa.

Iwo amaliza ndi kumumasula Chakwera ndi anyamata omupembedza kuti Chakwera alibe utsogoleri.

“Musazinyenge anthuni, muli ndi boma lomwe olitsogolera wake ndi panja ndithu. Alibe luntha la utsogoleri, alibe masomphenya, alibe ngakhale chikhumbokhumbo chosintha zinthu. Mkulu’yu alibe choti angapeleke, ndi panja. Uyu chimodzimodzi onse anachoka aja,” wamaliza motelo ndi ukali wake Chirwa.

Advertisement

One Comment

  1. Chakwera usiyd udindo siukukwanitsa pita mkachisi ukapitirize ntchito yako pochoka umtenge nzako chilimayo ndibodza lakero . umuwuze kuti bwanawe m’bola ine ndalawako koma iwe siuzakhalapo apa. Away nosense

Comments are closed.