Papangidwe kafukufuku wa momwe ndalama za Covid-19 zagwirira ntchito, yatero DPP

Advertisement

Chipani chotsutsa boma cha Democratic Progressive Party (DPP) chati ndichokhumudwa ndi malipoti oti nthambi ya boma yowona za ngozi zogwa mwadzidzidzi yagwiritsa kale ntchito ndalama pafupifupi K6.2 biliyoni polimbana ndi kufala kwa mliri wa Covid-19.

Mneneri wa chipanichi a Brown Mpinganjira kudzera mu uthenga omwe alemba ati iwo ngati chipani ali ndi umboni onse kuti pa 28 January nthambi yapadera yoyendetsa ntchito yolimbana ndi Covid yinayitanitsa akuluakulu aku DODMA kuti apeleke tsatanetsane wa momwe ndalama zayendela ndipo DODMA yinapeleka tsatanetsatane wa ndalama zokwana 595 miliyoni yokha m’malo mwa K6.2 biliyoni.

DPP yatiso pa mkumanowu zinaziwika kuti ndalama pafupifupi K15 miliyoni sizimaziwika kuti zinayenda bwanji ndipo DODMA yinapempha kuti awapase nthawi kuti akawelengetsere bwino  kaye.

DPP yati chokhumudwisa kwambiri ndi chakuti pa ndalama zomwe adayika kuti atetezele malire adziko lino, K580 miliyoni, pali malire adziko lino oti sakutetekezekanso monga Songwe ku Karonga.

Iwo atinso zomwe zachitikazi zikuwonetselatu kuti pali kusakazidwa kochuluka komwe anthufe sitikuziwa.

Iwo apa akumbutsa DODMA kuti ndalamazi eni ake ndi a Malawi omwe pano akhudzidwa zedi ndi mliriwu ndipo ndi chibwana zedi kusalabadila za anthu.

Apa iwo anamaliza ndikupempha kuti pakhale kafukufuku ndipo akatha ukapelekedwe ku nyumba ya malamulo m’masiku khumi ndi awiri ndipo ngati zizadziwike kuti zinasokonedzedwa malamulo a dziko lino adzagwire ntchito yake posawona nkhope.

Mliri wa Covid-19 ukupitililabe kutenga miyoyo ya anthu mu dziko muno ndipo pali chiyembekezo choti anthu okwana 750,000 posachedwapa alandila katemela oteteza kuti asatenge mliriwu.

Advertisement