Katemera sakhala okakamiza – boma

Advertisement

Boma la Malawi lati katemera wa mlili wa COVID-19 amene akuyembekezeka kufika mdziko muno kumathelo kwa mwezi uno sakhala okakamiza.

Izi ndimalingana ndi nduna yofalitsa nkhani a Gospel Kazako omwe amayankhula lachisanu pomwe akuluakulu a komiti yamtsogoleri wadziko lino yotsogolera pantchito yolimbana ndi COVID-19 amadziwitsa anthu momwe matendawa akhalira mmaola 24 apitawo.

Kazako

A Kazako anati boma likudziwa kuti anthu ambiri mdziko muno akuyankhula zambiri zosakhala bwino zokhudza katemera amene akuyembekezeka kuyamba kugawidwa kwa anthu kumayambiliro kwa mwezi wamawa.

Ndunayi yati ndizodabwitsa kuti anthu akukamba zambiri zolakwika zokhudza katemerayu chonsecho mdziko muno mmbuyomu komaso pano mwakhala mukubwera katemera osiyanasiyana koma anthu samayankhula kalikonse.

Apa iwo anati boma limakonda anthu ake ndipo anati silingavomere kuti mdziko muno mubwere katemera amene akhoza kuika pachiopsezo miyoyo ya anthu ochuluka ndipo alangiza anthu kuti asaope kali konse pankhani ya katemerayu.

“Titelo kuti katemera ameneyu sakhala okakamiza koma ife tikukhulupilira kuti anthu amene amafunira anzawo zabwino azabayitsa katemela ameneyu chifukwa kukana kubayitsa katemerayu kukhala kuika miyoyo ya azibale anu pachiopsezo.

“Abale anga musakhale ndimantha, katemera uyu ndiwabwino bwino, abale athu akomkuno avomereza kuti katemerayu ndiwabwino. Ubwino wake maiko akunja akulandira kunoso tikulandira, nde inu mukuopa chiyani? Boma lanu silingakatenge dziphe kwina kakwe mkubweretsa kuno,”atelo a Kazako.

A Kazako anatiso ngakhale nduna zaboma nazo zidzalandira nawo katemera ameneyu ndipo alimbikitsa anthu kuti achotse mantha pankhani ya katemerayu ponena kuti siwoopsa monga anthu akunenera mmakwalalamu.

Iwo awonjezeraso kuti akuluakulu aboma panopa akhala akumafusa anthu zomwe sakumvetsa bwino pankhani ya katemerayu ndipo alangiza anthu onse omwe ali ndi mafuso pankhani yakatemerayu kuti alifuse bomali ndipo liwayankha.

Pakadali pano mmaola 24 apitawa, anthu 497 atsopano achira kumlili umenewu pamene anthu 476 atsopano apezeka ndi kachirombo ka kolona ndipo mmaola 24 amenewa anthu 20 ndi omwe amwalira.

Advertisement