Akweza ma koleji a APM aja

Advertisement

Ife Tonse amene tinachita ngati mwayi wa ku yunivesite sunatipeze, ife aja a Mutharika anatikonzela ma koleji a tekiniko mmakwalalamu, boma la Tonse latipeza litilankhule. Lili ndi uthenga koma okhumudwitsa.

Unduna wa za ntchito walengeza kuti tsopano mtengo olipila mu sukulu za tekiniko mu dziko muno wakwela.

Malinga ndi chikalata chimene undunawu watulutsa pa 21 January, mitengo yolipila mu sukulu zonse zophunzitsa maluso osiyanasiyana ndi ntchito zina za manja wakwela.

Malinga ndi chikalata chochoka ku undunawu, sukulu za tekiniko za dziko lonse ndizo zikhale zokwela kwambili.

“Tsopano ophunzila mu sukulu zimenezi (zimene pa chingelezi zimatchedwa national technical schools) azilipila MK50, 000,” chatelo chikalatachi.

Anthu onse ophunzila mu sukulu za tekiniko za mu madera, chitukuko chimene chinabwela ndi mtsogoleri opuma a Peter Mutharika, ati tsopano azilipila MK12, 500 pa Mwezi kuchoka pa MK3000 imene amalipila kale. Awa ndi ophunzila amene mbali ina boma limawalipilila.

Ndipo sukulu zonse zophunzitsa maluso osiyanasiyana za mu mmakwalala ati nazo zakwela kuchoka pa MK3000 kufika pa MK8000.

Boma lakweza mtengo wa sukuluzi pano pamene umphawi waluma a Malawi ochuluka kamba ka mlili wa coronavirus.

Advertisement

One Comment

Comments are closed.