Ambiri akumachira akabwera kuchipatala – mkulu wa chipatala cha Queens

Advertisement

Mkulu wa chipatala cha Queen Elizabeth mumzinda wa Blantyre walangiza anthu m’dziko muno kuti asakhale ndimantha kupita ku chipatala pomwe akudwala poopa kukawapeza ndi matenda a COVID-19 ndipo ati si aliyense akumamwalira akapita kuchipatala poti ambiri akumachira.

Dr Samson Mndolo ati kafukufuku akusonyeza kuti a Malawi ambiri ayamba kuopa kupita kuchipatala pomwe sakumva bwino mthupi ati kaamba koopa kuti akapitako akakamizidwa kuyezedwa matenda a COVID-19.

Apa a Mndolo anati ndizodandaulitsa kuti anthu akufalitsa mbiri yoti aliyense yemwe akumapita kuchipatala akumamuuza kuti akudwala COVID-19 zomwe anatiso ndikuipitsa mbiri ya zipatala za mdziko muno.

Iwo ati anthu akuyenera kudziwa kuti anthu ambiri omwe akudwala matenda a COVID-19 akuchira ndipo sikoyenera kuti anthu azingokhala m’makomo mwawo osapita kuchipatala pomwe akudwala matenda osiyanasiyana.

A Mndolo anaonjezera kuti mchitidwe osafuna kupita kuchipatala powopa kukayezedwa COVID-19 wapangitsa kuti chiwerengero cha anthu omwe akumwalilira m’makomo chikwere kwambiri.

Mkuluyu watiso kaamba ka mchitidwe osafuna kupita kuchipatalawu zipatala zambiri zikumalandira anthu oti amwalira kale ati kaamba koti anthu akumazikakamiza kupita kuchipatala madzi atafika mkhosi.

“Tikupitilizabe kulandira odwala ochuluka chifukwa chamatenda a COVID-19 koma nkhani yabwino ndiyoti anthu ambiri akuchira. Chomwe taona n’chakuti anthu ambiri akumabwera nawo kuchipatala atamwalira kale, enaso akumangokhala pang’ono nchipatala kenaka mkumwalira.

“Zikuonetsa kuti anthu kunyumbako akuchita mantha kubwera kuchipatala, ena akumauzana kuti aliyese opita kuchipatala akumamwalira, enaso akumati kuchipatala kulibe malo, izi sizoona ndipo ndikuwalimbikitsa anthu kuti azipita kuchipatala nsanga pomwe akudwala,” atelo a Mndolo.

Iwo anati pafupifupi tsiku lililonse anthu ochuluka akumachira kumatendawa ndipo anati ndi anthu ochepa okha omwe akumamwalira zomwe anati ziziwapatsa chilimbikitso anthu kuti ngati atatsata malangizo azachipatala bwino bwino, atha kuchira matendawa mosavuta.

A Mndolo ati pakadali pano akuluakulu a chipatalachi akufuna ayambitse gulu la anthu omwe anachira ku matenda a COVID-19 ndicholinga choti anthuwa azipelekera umboni oti matendawa ndiochizika.

Advertisement