Tufuna kwathu: chipolowe ku Blantyre pamene ma tchona a ku Sosa Afrika akukana kusungidwa

Advertisement

Ma tchona ochokela mu dziko la South Africa anavuta kwa mnanu mu boma la Blantyre pamene anatseka mseu wa pakati pa Zomba ndi Blantyre kuli kukana kuti asungidwe ndi boma pa sukulu yophunzitsa oyang’anila ndende pa Mapanga.

Malinga ndi mtolankhani wathu, ma tchona’wa anafika pa ma bus ochokela ku joweni ndipo malingana ndi malamulo a tsopano akuyenela kufikila ku malo opangidwa ndi boma kuti asungidwe kudikila zotsatila zawo za coronavirus.

Koma iwo atatengeledwa ku Mapanga ndi kudziwitsidwa kuti asungidwa kaye ndinso kulandidwa ziphaso zoyendela, anachita ukali ndi kuyamba kuponya miyala mu mseu mpaka kuswa galimoto za anthu odutsa.

A polisi anathamangila ku maloku komwe anathila utsi okhetsa msozi kuti akhazikitse bata.

Mu dziko la South Africa mwavuta mlili wa Covid umene tsopano wakhutukila nawo mu dziko la Malawi.

Ngati njila imodzi yofuna kupewa kufala kwa matendawa, boma lalamula kuti onse obwela mu dziko muno azisungidwa kaye mpaka ndi kuyesedwa ngati alibe kachilombo ka coronavirus asanawalole kubwelela kwawo.

Advertisement