Wavuta Covid-19, Chakwera wabisala

Advertisement

Ali kuti a Chakwera okonda kuyenda ndi kuyankhula ndi ife ana awo pano pamene nyanja yakalipa ndi ukali wa Covid-19? Akudabwa chomwecho a Malawi pamene chiwelengelo cha anthu opezeka ndi Covid-19 chikuchulukila.

Adindo amene akutsogolela pa nkhondo yolimbana ndi mliri wa Covid-19 alengeza kuti Malawi yagwidwa malo oipa ndi mliriwu. Malinga ndi mkulu amene akutsogolela nkhondoyi a Dr John Phuka, tizilombo tachilendo toyambitsa nthendayi tsopano tafika ku Malawi.

“Tizilombo timeneti ndi taukali,” anatelo a Phuka. “Tikupangitsa nthendayi kufala msanga, kugwila achichepele ndipo ikudza ndi ukali.”

Monga mwa mawu awo, mu masiku atatu otsatizana Malawi wakhala akugwidwa ndi mantha maka akalengeza nambala za anthu opezeka ndi matendawa.

Mwachitsanzo lachisanu, anthu oposa mazana atatu (300) anapezeka ndi matenda wa atayesedwa pomwe anthu asanu anamwalila.

Koma pamene zinthu zili chonchi, mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera sanayankhulepo kwa mtundu wa a Malawi kuti awunikile njira ndi kupeleka chilimbikitso.

A Malawi ena adabwa kuti a Chakwera athawila kuti mu nyengo yofunika ngati ino.

Advertisement