Bambo wina waphedwa ku Dowa atamupeza akuchita za dama ndi mkazi wa mwini

Advertisement
Malawi24.com

Apolisi m’boma la Dowa amanga bambo Andrew Makanjira a zaka 45 powaganizira kuti apha bambo wina yemwe a Makanjirawo anamupeza akuchita za dama ndi mkazi wawo.

Bambo wophedwayo ndi a Yekomia Weston James.

Malingana ndi m’neneri wa apolisi ku Dowa a Gladson Mbupha, malemuwa adapita kumaliro ndi azichimwene awo awiri ndipo pobwelera kumaliro iwo adatsika galimoto kuti akufuna akawone mzawo wina mu dera la Nyalubwe.

Powona kuti masiku akutha koma m’bale wawo sakubwera mchimwene wa malemuwa a Jepheter Saona adapita m’mudzi omwe iwo ankanena kuti akupitako koma sadawapeze.

Apa ndi pomwe iwo adakanena ku Polisi ya Mtengo wa nthenga.

Sabata lino Apolisi analandila uthenga kuti kwapezeka munthu wakufa mu Ngalande m’mudzi wa Kanjondo, pomwe achibale amalemuwa adapita kukawona thupi adatsimikiza kuti adali m’bale wawoyo.

Apolisi aku Dzaleka atafufuza anamanga Andrew Makanjira powaganizira kuti ndiwo adachita izi.

Atawafunsa, iwo anavomera kuti ndiwo adapha a Makanjira atawapeza akuchita za dama ndi mkazi wawo.

Oganizilidwawa akawonekera ku bwalo la milandu posachedwapa.

Advertisement

One Comment

Comments are closed.