Munakondwa ndi Kondwani? Kwabwela Dalitso ku DPP

Advertisement

Akupitadi adad kutula pansi udindo mu chipani cha DPP, koma sikuti udindo amusiyila chabe Kondwani Nankhumwa uja wakhala akuchititsa misonkhano ngati mwini wachipani. Kuli mpikisano tsopano pamene mkulu wakale wa banki yaikulu mu dziko muno a Dalitso Kabambe alengeza kuti nawo akufuna utsogoleri wa DPP.

A Dalitso Kabambe amene anachotsedwa ndi boma la a Lazarus Chakwera pa mpando wawo alengeza lero ku likulu la chipani cha DPP ku Blantyre kuti iwo tsopano ajowina chipani cha DPP ndipo apanga ndale.

Malipoti akuti a Kabambe akukonzekela kuti atenge chipani cha DPP ndi kuimila pa mpikisano wa President mu chaka cha 2025 pamene dziko lino likuyenelanso kuchita chisankho.

A Kabambe akhala akugwila ntchito mu boma kuyambila mu chaka cha 1998 pamene anamaliza sukulu yawo ya ukachenjede. Mu chaka cha 2017 iwo anasankhidwa kukhala mkulu wa Banki yaikulu mu dziko muno, Reserve Bank pa chingerezi. Mu nthawi yawo, ma bungwe ndi akadaulo oona za chuma anawayamikila kuti chuma cha Malawi chimayenda bwino.

Pofuna utsogoleri wa DPP, a Kabambe akuyenela kupikisana ndi nkhalakale za chipani monga a Kondwani Nankhumwa amenenso ndi wachiwili kwa mtsogoleri wa chipanichi mu chigawo cha Kummwera. A Nankhumwa akhala kale akuzipeleka ngati mtsogoleri wa chipani cha DPP kuyambila pamene chinagwa pa chisankho cha chibweleza chaka chikungothachi.

 

Advertisement

One Comment

Comments are closed.