Kukhala ndi chilakolako chofuna kugona ndi mwana ndi vuto la ubongo

Advertisement

Dotolo wa mavuto akaganidwe ka anthu wati munthu wamkulu kukhala ndi chilakolako chofuna kugona ndi mwana ndi vuto la matenda a kaganizidwe koma ambiri samadziwa kuti ili ndi vuto loti atha kuthandidzidwa kuchipatala.

Izi zikudza pomwe dziko lino likulimbana ndi mchitidwe ogwililira ana ndi amayi omwe ukukulirakulira ngakhale boma ndi mabungwe akupitirizabe kuphunzitsa anthu kuyipa kwa mchitidwewu.

Solomon Chomba

Anthu ogwilirawa nthawi zambiri ku bwalo la milandu amapempha khoti kuti liwakhululukire chifukwa sakadziwa  chomwe amachita.

Polankhula ndi nyuzipepalayi, Solomon Chomba  yemwe amagwira ntchito pa chipatala cha boma ku Mzuzu ku nthambi ya ubongo wati munthu kukhala ndi chilakolako chogonana ndi mwana ndi vuto loti atha kuthandizidwa kuchipatala kuti ayambenso kuwona ana ngati ana osati akazi.

Iye anapitilizatso kupempha achinyamata ndi azibambo kuti asachite manyazi kupita ku chipatala akawona kuti akumakhala ndi maganizidwe oterewa kuti akalandile thandizo.

Dziko lino malamulo aakulu amaloleza munthu kuyamba zogonana ngati wakwanisa zaka 18 ndipo kugona ndi mwana ndi mlandu.

Maziko Matemba

Katswiri waza umoyo  m’dziko muno a Maziko Matemba  ati dziko lino liyeneranso kuwunikira ndondomeko zake pa nkhani yakaganizidwe ka anthu ponena kuti ku mayiko akunja ena amatha kumuwunika kaye munthu kaganizidwe kake asanapeleke chilango.

Iye anapitiliza kuti nthambi yapadera yomwe boma likufuna kukhazikitsa kuti liwunikire chomwe chikukolezera zogwilirira ana liwonanso ndondomeko yowunikira kaganizidwe ngati vuto lofunikira thandidzo mwamsanga.

 

Advertisement