Agamulidwa zaka zisanu kamba kogwililira ana anayi

Advertisement

Bwalo la milandu m’boma la Dowa lalamula bambo wina wa zaka 21 kukakhala kundende zaka zisanu kaamba kopezeka olakwa pamlandu ogwililira anyamata anayi.

Watsimikiza zankhaniyi ndi ofalitsa nkhani pa polisi ya Dowa a Sub Inspector Gladson M’bumpha omwe azindikira mkuluyu ngati a Innocent Poita.

Malingana ndi a M’bumpha, bambo Poita akhala akugwililira anyamata anayiwa kuyambira chaka cha 2016 kufikira pa 19 November chaka chino pomwe anagwidwa ndikumangidwa.

Nkhaniyi ikuti anyamatawa omwe ndi azaka pakati pa 10 ndi 17 amamupeza kunyumba kwake komwe amapita kuti akawonere makanema pa lamya yamkuluyu.

Anyamatawa akafika kunyumba kwake, mkulu wantima osaugwilayu amawanyengelera mpaka amagonana nawo kufikira mwezi watha pomwe nkhaniyi inaululika ndipo Poita anamangidwa.

Ataonekera kubwalo lamilandu, bamboyu anavomera mlanduwu koma anapempha bwalo lamilandulo kuti limuchitile chifundo pomupatsa chilango chofewa ati kaamba koti amayang’ira ana amasiye komaso anati ali ndi banja lomwe limadalira iyeyo.

Koma yemwe amaimilira boma pa mlanduwu a Sub Inspector Ezra Bakili anatsutsa mwantu wagalu pempho labamboyu ponena kuti mlanduwu ndiwaukulu ndipo mkuluyu akuyenera kulandira chilango chokhwima kuti likhale phunziro kwa enaso omwe ali ndimaganizo oyipa ngati amenewa.

Ndipo popeleka chigamulo chake, oweruza milandu a Magistrate Amran Phiri anagwirizana ndi a Bakili ponena kuti bambo Poita apanga zinthu zochititsa manyazi kwambiri zomwe mkulakwira malamulo adziko lino komaso kuipitsa chikhalidwe cha anthu mdziko muno.

Apa a Phiri analamura kuti mkuluyu akakhale kundende zaka zisanu ndikukagwira ntchito yakalavura gaga.

Bambo Innocent Poita amachokera mmudzi mwa Ndalama, mfumu yaikulu Chiwere ku Dowa.

Advertisement