Ogwililira azimenyedwa kaye – nduna yazachitetezo

Advertisement

Pomwe dziko la Malawi lili mkati mopeza njira zothanilana ndikukula kwamchitidwe ogwililira, yemwe ndinduna yowona zachitetezo m’dziko muno a Richard Chimwendo Banda awuza anthu kuti azimenya wina aliyense opezeka atagwililira.

A Chimwendo Banda amayankhula izi Lamulungu lapitali pa 29 November pomwe anachititsa nsonkhano pa bwalo la zamasewelo la Chantulo kumadzulo kwaboma la Mangochi.

Pamsonkhanowu nduna yazachitetezoyi inauza anthu omwe anasonkhana pamalowa kuti mchitidwe ogwililira ukukula chifukwa choti anthu ogwililira sakumakumana ndi mazangazime akagwidwa.

Iwo anati zikumakhala zokhumudwitsa kumuona munthu atagwidwa kaamba koganizilidwa kugwililira koma akuyenda bwinobwino osamenyedwa ndipo iwo alamula anthu kuti azimuonetsa chidameta nkhanga mpala oganizilidwa aliyese.

Apa ndunayi yati ikufunitsitsa kuti oganizilidwa kugwililira aliyese akamakasiyidwa mmanja mwa apolisi, apolisiwo adzidziwa kuti munthuyo walangidwa kale.

“Aliyese ogwililira akamafika ku polisi tikufuna tidzidziwa kuti mwachita naye kale. Ndatitu ogwililira mwana yekha eti? Wakuba muzimutenga ndikupita naye ku polisi koma ogwililira mwana menyani makofi, tibulani.

“Zafika panyasi, kumugwira munthu alibwino bwino alimya koma chosecho akuti anagwililira mwana, iyayi, community polisi igwile ntchito tsopano ndipo mafumu mulumikizane ndi apolisi ammudzi kuthana ndi zimenezo.” atelo anduna a Banda.

Pakadali pano anthu adzudzula mawu andunayi ati ponena kuti izi zitha kuonjezera mchitidwe otengera malamulo mmanja mwawo ndipo anthu ambiri atha kuphedwa kaamba ka mawu andunayi.

Anthu ati a Chimwendo Banda ngati nduna yachitetezo m’dziko akuyenera kumalimbikitsa anthu kuti azitsata malamulo osati kulimbikitsa anthu kuti azitengela malamulo mmanja mwawo zomwe anthu ambiri ati zitha kulowetsa chisawawa m’dziko muno.

Advertisement