Mwini munda anyotsoledwa khutu ndi mlonda


Bambo wa zaka 37 ku Neno akuvutika ndi bala lomwe linadza mlonda wina atamuluma khutu lake pomwe mlondayo ankafuna kulanda munda wa a Walani.

Bamboyu Jones Walani akudandaulaso kuti sakudziwa komwe kuli khutu lonyotseledwalo.

Bamboyu wauza Malawi24 kuti pa 14 November analumidwa khutu mpaka kunyosoka ndi muthu wina yemwe amkamuzulira mbewu ku dimba. Munthu olumayo ndi mulonda waku agriculture ku Neno komweko.

Malingana ndi a Walani, onsewa amakhala pa nyumba za Agriculture ku Neno ndiye iwowa a Walani anayamba kulima ku dimba pafpi ndi nyumba yawo.

A Walani

Mlondayu powona zimenezi, amafuna kulanda dimbalo ndiye anayamba kuzulu zomwe a Walani anadzala. Izi zinadzetsa mkangano mpaka mlondayu anafika poluma khutu la a Walani.

Mabwana a anthuwa ku Agriculture ya ku Neno amafuna aphiphiritse nkhaniyi powopa kuti alonda aja achotsedwa ntchito.

Koma mlondayo anamangidwa lamulungu pa 15 ndipo analowa mu khothi lolemba pa 15.

“Mlondayo anabvomela mlandu koma chomwe chinandidabwisa ndichokuti, sindinapasidwe mpata oyakhula, ndipo judge anagamula kuti ndipasidwe K160,000 ndipo ndalamayo inaperekedwa K40,000 ndipo muthuyo anamutulusa,” anatero bamboyu.

A Walani akudandaula kuti chilungamo sichinaoneke chifukwa akuvutika komanso  sakudziwa kuti khutulo mlondayo analidya kapena anapanga nalo chani zomwe zinapangitsa kuti lisakosekedweso kuchipatala.

Malingana ndi a Walani, akufuna thandizo kuti chilungamo chiwoneke popeza ndala zomwe anapatsidwa ndi zochepa kutengera bala lawo.

“Ma bwana a ku agriculture sanabwereko kuzandiwona olo kuyimba foni, ndikubvutika ndi bala lomwe likunditengera ndalama zambiri,” anatero bamboyu.

Discover more from Malawi 24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading