Paulo ndi Sila? Wabanduka Bushiri pa Joweni

Bushiri Major 1

Kusiyana kwake sanapemphele, zitseko zandende sizinatseguke zokha, koma pamapeto pake moyo wake naye wasangalala.

Amene amazitcha kuti mneneri ndipo ali ndi luso lodziwa za mtsogolo, Shepherd Bushiri, wathawa mu dziko la South Africa kumene amayankha milandu yokhudzana ndi kuba mwa chinyengo ndalama.

Bushiri amene amatchukanso kuti Major1anapatsidwa belo pa bwalo ndipo analandidwa ziphaso zoyendela limodzi ndi mkazi wake. Koma mu nkhani yozizwitsa mutu, loweruka mmawa Bushiri analengeza kuti iye wachoka mu dziko la South Africa.

Major 1 Mary Bushiri Money Laundering Fraud
Paulo ndi Sila? Wabanduka Bushiri

“Ndafuna ndikudziwitseni kuti ndabwelela kwathu ku Malawi,” analemba choncho Bushiri. “Pa Joweni anthu amafuna kundipha ndipo boma lawo silimafuna kunditeteza. Amangondiyimba milandu yopanda mitu, ina yoti amayenela aziyimbana okhaokha.”

Bushiri anapitilizanso kunena kuti iye ndi okonzeka kubwelelanso ku South Africa ngati atatsimikizilidwa kuti chitetezo chake chikakhalapo ndipo mulandu wake ukaona chilungamo chikuyenda ngati madzi.

“Asinthe anthu ondiyimba mulandu ndipo anditsimikizile kuti ndikapitako sindikatsekeledwanso mu chitolokosi ndiye ndipitanso,” watero Bushiri.

Chadabwitsa anthu ndi choti Bushiri wabwela ku Malawi molingana ndi mtsogoleri wa dziko Lazarus Chakwera amene naye adakayenda mu dziko la South Africa.

Advertisement

One Comment

  1. Chakwera ndamene anadzamutenga amatero walandira kanganyase afotokoze bwino, bushiri akwera bwanji presidentiam jet? Ngati ndani?

Comments are closed.