Coronavirus sanathe tisatayilire – Phuka

Wapampando wa gulu komwe linakhazikitsidwa ndi mtsogoleri wa dziko lino pantchito yolimbana ndi kufala kwa mlili wa COVID-19, John Phuka, walangiza anthu kuti asasiye kutsata njira zopewera nthendayi.

Izi ndimalingana ndi wapampandoyu a John Phuka omwe anayankhula ndinyumba zina zoulutsira mawu Lolemba pomwe amapeleka chithuzithuzi cha mmene zinthu zilili pantchito yolimbana ndikufala kwa matenda wa.

A Phuka ati ndizokhumudwitsa kuti pali anthu ena mdziko muno omwe akuona ngati mlili wa COVID-19 watha ndipo ati anthu ambiri asiya kutsaso malamulo omwe boma linakhazikitsa komaso njira zina zaukhondo.

Iwo ati anthu akuyenera kudziwa kuti nthenda yi inakali ndi mphamvu angakhale kuti pano chiwelengero cha anthu opezeka ndikachilombo ka Coronavirus kakumka kakutsikira tsikirabe.

“Coronavirus sanathe chifukwa mutha kuwona kuti lero tapezaso anthu ena odwala zomwe zikusonyeza kuti nthendayi idakalipo pakati pathu koma anthu ena sakutsatira njira zopewera nthendayi.

“Choncho tikupempha ndithu kuti anthu alimbikire kuchita zonse zopewera nthendayi ndicholinga choti mxliliwu utheretu mdziko muno,” anatero Phuka.

Angakhale zili chomcho, a Phuka ayamikira anthu ena omwe akupitilizabe kutsatira ndondomeko zonse zothanirana ndi mliliwu ndipo apempha onse anasiya kutsatira njirazi kuti ayambireso.

Lolemba anthu ena atatu apezekaso ndikachilomboka mmaola 24 apitawa zomwe zapangitsa kuti chiwelengero cha anthu onse omwe apezeka ndi nthenda yi m’dziko muno chifike pa 5,860.

Pakadali pano chiwelengero cha anthu amwalira ndi nthendayi chinakali pa 181 pomwe chiwelengero cha anthu omwe achira chafika pa 4,757 kutsatira kuchira kwa anthu 15 zomwe zapangitsa kuti chiwelengero cha anthu omwe akudwalabe nthenda yi chifika pa 922 ndipo anthu 58,002 ndi omwe ayezedwa chiyambireni nthendayi.

Advertisement