Chipasupasu ku DPP: Nankhumwa ndi ena atatu athotholedwa

Chipasupasu chayang’ana chipani chotsutsa boma cha DPP pomwe chalengeza kuchotsedwa mchipanimu kwa wachiwiri kwa mtsogoleri wachipanichi mchigawo chakum’mwera a Kondwani Nankhumwa komaso akuluakulu ena atatu.

Watsimikiza za nkhaniyi ndi mneneri wachipanichi a Brown Mpinganjira omwe ati a Nankhumwa achotsedwa limodzi ndi mlembi wakale wachipanichi a Grezeldar Jeffrey, a Jappie Mhango omwe anali msungi chuma komaso phungu wachipanichi ku Mulanje a Yusuf Nthenda.

A Mpinganjira ati ganizo lochotsa anthuwa labwera kutsatira mkumano omwe akuluakulu achipanichi anachititsa kunyumba kwa mtsogoleri wachipanichi a Peter Mutharika ku Mangochi lachisanu.

A Mpinganjira ati akuluakulu achipanichi anapeza kuti a Nankhumwa pamodzi ndi amzawo omwe awachotsawa akhala akuphwanya ena mwa malamulo achipanichi ndipo anati imodzi mwa nkhani zake ndi yaudindo wa mtsogoleri wazipani zotsutsa ku nyumba yamalamulo.

“Nkhani yoti anthu anayi achotsedwa mumchipani imeneyo ndiyowona. Komiti yaikulu yachipanichi inakumana kukambirana zinthu zomwe zakhala zikuchitika mu chipani chathu cha DPP.

“Choncho malipoti omwe anapelekedwa, komitiyi inaona kuti anthu amenewa aphwanya malamulo achipani chathu ndipo nkwabwino kuti awatulutse mu nchipanichi.” anatero Mpinganjira.

A Mpinganjira anatsimikiza kuti pano chipanichi chasankha chasankha a Joseph Mwanamvekha omwe alowa mmalo mwa a Nankhumwa paudindo wa wachiwiri kwa mtsogoleri wachipanichi mchigawo chakummwera.

Chipanichi chatiso chasankha a Samuel Tembenu kulowa mmalo mwa a Jeffrey kukhala mlembi wankulu wachipanichi pomwe a Nick Masebo alowa mmalo mwa a Mhango paudindo wa msungi chuma.

Pakadali pano a Kondwani Nankhumwa sanayankhule pankhaniyi koma ati ayankhula akalandira kalata yowauza za nkhani yi kuchokera kwa akuluakulu achipaniwa koma mphekesera zikusonyeza kuti a Nankhumwa atha kuyambitsa chipani chawo.

Chipani cha DPP chakhala chogawanika kuyambira pomwe chinaluza chisankho chapadera chomwe chinachitika pa 23 June chaka chino pomwe khothi linalamura kuti chisankho cha chaka chatha sichinayende bwino

Advertisement