‘Osaleka kutsatira ndondomeko zopewera Covid-19’

Advertisement

Anthu m’dziko muno awapempha  kuti asalekelere kutsatila ndondomeko zomwe a zaumoyo anakhazikitsa zopewera muliri wa Covid 19.

Nkhawazi zadza pomwe pomwe Malawi 24 idakayendela town ya Kasungu m’mawa lero pomwe yinapeza kuti eni sitolo komanso ogula  sakutsatila komwe ndondomeko zomwe zinakhadzikitsidwa kupewera matendawa  ndi aza umoyo m’dziko muno pomwe boma silinalengeze kuti muliliwu watha.

Mkulu wa bungwe lomenyera ufulu waza umoyo la Malawi Health Equity Network (MEHEN) a Joel Jobe  ati eni Sitolo komanso ogula akumbukire komwe m’mene zinaliri m’mbuyomu ndi nthendayi ndipo ndichibwana cha mchombo lende kusatsatira ndondomeko.

Iwo anapitiliza kuchenjeza eni sitolo kuti kusatsatira ndondomeko kuli ndikuthekela kochotsa chikoka pama bizinesi awo kaamba anthu adziwopa kukatengako matenda poti nthendayi siyinathe ndipo anthu akupitililabe kuyitenga.

Apa iwo anapempha munthu payekha payekha kuti adzitsatira ndondomeko .

Nawo a Maziko Matemba omwe amalankhulapo pankhani za umoyo ati kusasatira ndondomekozi kuli ndikuthekela kosokonedza ntchito yonse yolimbana ndi nthendayi ndipo achenjeza anthu kuti akhale tcheru poti nthendayi itha kupsyespya aliyense m’dziko lino ngati anthu sakusamala.

Apa a Matemba anatengelapo mwayi kupempha boma kuti alimbikitse anthu kupewa nthendayi poti ikupululabe miyoyo ya anthu.

Advertisement