ACB ikuchita chidodo pa milandu ya katangale, atero a HRDC

Advertisement

Bungwe lomenyera ufulu wa anthu mdziko muno lotchedwa HRDC lati bungwe lolimbana ndi katangale la AntI-Corruption Bureau (ACB) likuchita chidodo.

Wapampando wa bungweli a Gift Trapence polankhula ndi olemba nkhani lero m’mawa anati bungwe lawo likupitilizabe kutsinidwa khutu ndi anthu akufuna kwabwino pa za katangale ndi ziphuphu zomwe zimachitika ndi boma lakale.

A Trapence anapitilila kufotokoza kuti iwo anatula mphekeserazi ku bungwe lothana ndi katangale la ACB koma a bungweli akuchita chidodo kuwunika nkhanizi.

Apa iwo anapempha bungwe la ACB kuti likhazikitse nthambi yapadera yofufuza nkhanizi kuti aphyede mwachangu.

A Trapence anapitiliza kunena kuti maso awo ali tcheru kuwona momwe boma lakadali panoli likuyedetsera ntchito zake kuti pasakhale ukathyali uli onse.

Atafusidwa kuti afotokozepo iwo ngati bungwe momwe awonela bomali, a Trapence anati a Malawi eni ndi omwe athilepo maganizo kudzera munjira zomwe iwo ngati bungwe akhadzikitse m’masiku akudzawa.

Malingana ndi a Trapence, bungwe lawo likufuna a Malawi anenepo momwe aliwonela boma la Tonse Alliance m’masiku 100.

Advertisement