Mafumu apempha boma likonze ziliza za azungu awiri

Advertisement

Mafumu ku Chiradzulu adandaula ndikusasamalidwa kwa ziliza za a William Jervis Livingstone komanso Duncan McCormick omwe adaphedwa ndi a John Chilembwe mu nthawi ya utsamunda.

Iwo ati mandawa ali ndi mbili yosaiwalika komanso yofunikira kwambili ku dziko lino chifukwa awiriwo anaphedwa nthawi yomwe a Chilembwe ankamenyera ufulu wa dziko lino mu chaka cha 1915.

Mandawa komanso nyumba ya azunguwa zili ku Magomero ku dela la mfumu ya ikulu Ntchema, m’mudzi mwa mfumu ya ing’ono Mitawa.

chiliza cha a McCormick

Mfumu yaikulu Ntchema yati ndi yodandaula kwambili ndikusasamalidwa kwa zilizazi chifukwa mandawa ali ndi mbiri yosaiwalika ku dziko lino la Malawi.

Iwo ati mandawa komanso nyumba yomwe amakhalamo a Livingstone zili ndi kuthekela komabweletsa ndalama ku boma.

“Manda amene aja komanso nyumba yomwe amakhalamo Livingstone zili ndi kuthekela komabweletsa ndalama zochuluka ku boma ku boma.

“Nyumba ija itati ikonzedwe, ndikuipanga kuti ikhale lodge boma litha kumatolela ndalama zochuluka za mziko mommuno komanso zakunja,’’ anatero a Ntchema.

Chiliza cha a Livingstone

Pomaliza mfumuyi inadandaula kuti zaka za m’mbuyomu adalipempha boma kuti likonzeso malowa makamaka manda a William Jervis Livingstone komanso Duncan McCormick koma palibe chomwe chinachitika mpaka pano.

Mfumu yaing’ono Mitawa, inathililapo ndemanga pa zomwe Mfumu yaikulu Ntchema inanena, iyo inati amalandila alendo osiyanasiyana omwe amabwela kuzaona malowa.

Mfumuyi yadandaula kuti chomvetsa chisoni ndi choti malowa ndiosasamalilika konse, inati malowa akumvetsa chisoni ngati alibe mbiri.

“Timakhala tikulandila alendo osiyanasiyana kuchokelanso madela osiyanasiyana kubwela m’mudzi mwanga muno kuzaona manda ndi nyumba ya a Livingstone.

“Chomvetsa chisoni ndi choti ngakhale mandawa ali ndi mbili yaikulu kwambili, malowa ndi osasamalilika komwe moti mandawo akakhalabe m’mene alili muzaka zikubwelazi azafafanizika.

“Moti m’badwo ukubwelawu uzizangomva kuti kunali manda a Livingstone kuno koma osawaona mandawo choncho pempho langa ku boma ndi loti atati akonze malowa mbili ingalemekezeke,’’ inatero mfumu yaing’ono Mitawa.

Advertisement