Apolisi apulumutsa Gogo  ku Thyolo

Malawi24.com

Chipwilikiti chinabuka m’mudzi mwa Molande, Mfumu yaikulu Nchilamwera m’boma la Thyolo komwe apolisi alandisa gogo wina m’manja mwa anthu okwiya omwe amafuna kumupha pomuganizira kuti ndi mfiti.

Chinautsa mapiri pa chigwa nchakuti la Mulungu pa 6 mwezi uno mnyamata wina anapita kukasambila ku damu la Nchima estate ndi anzake komwe mnyamatayo anafera pa damupo koma mtembo sukuoneka.

Poyakhulapo mfumu Molande, ati iwo anali odabwa kuona gogo oganizilidwayo akuwauza kuti amuteteze.

“Chomwe chachitika ndichoti pa 6 September 2020, pa banja lina mnyamata wamkulube ndithu anasowa pa damu koma mpaka lero thupi lake silinapezeke. Koma mphekesera zikumveka kuti pa mtundu pawopo pali kukaikilana kuti azigogo ena ndi amfiti.

“Chifukwa sikoyambayi, sabata ziwiri zapitazi kunasowaso anyamata motsatizana ndipo aka mkachitatu. Nde kucha kwa lero gogoyi anandipeza kuti ndimuteteze kenako chakumasanaku ndinangoona chikhamu cha wanthu kumakuwa kuti ndimutuluse,” a Molande adafotokoza.

Koma iwo pofuna kuteteza moyo wa gogoyo anaimbila apolisi ndipo apolisi osachepera asanu ndi atatu anafika pamalopo.

Pofuna kubalalisa khamulo, apolisi adaomba mfuti ya utsi okhesa misozi kenako mkumutenga gogoyo kupita naye ku polisi.

Apolisi anati ayakhabe za khaniyi. Koma pakadali pano apolisi a PMF apitaso ku damuko kuti akayang’ane thupi la mnyamatayo.

Advertisement