Tabitha Chawinga awumbuzidwa ndi mphwake

Advertisement

Katswiri okankha chikopa mu timu ya   mpira wa miyendo ya fuko lino Tabitha Chawinga adaona ngati kumaloto loweruka lapitali pamene mng’ono wake Temwa Chawinga  adamuonesa zakuda.

Tabitha adalephera kuithandiza timu yake ya Jiangsu Suning kupeza chipambano mu ma sewera awo amene amkakumana ndi team ya Wuhan Jiangda yomwe amasewera Temwa, mu dziko la China.

Jiangsu idalephera masewera wo ndi zigoli zitatu kwa du. Izi zidali choncho ngakhale Temwa sadalione golo.

Polankhula ndi Nyuzipepala ya chilokolo, Temwa adati iye ndiokondwa kuti adakwanisa kupambana masewero awo. Iye adatinso timu ya Jiangsu idamumaka koophya zomwe zidapereka mpata kwa osewera anzake kuti apeze mwayi omwesa zigoli.

Kumbali yake, Tabitha adati ndiokhumudwa ndikulephera kupambana patapita nthawi yaitali chilephelereni pa masewero a mpira.

Tabitha ndi osewera amene adachita bwino mu chaka chathachi mu dziko la China. Anapambana mphoto zitatu posewera bwino kwambiri mu mpikisano wa dzikolo komanso pomwesa zigolo zambiria kuposa wina aliyese.

Advertisement

One Comment

Comments are closed.