M’busa, Sheikh ayankhulapo pa kuchotsedwa kwa chikwangwani


M’busa Wilson wa tchalichi cha Good Samaritan komanso Sheikh Hussen Abdul Kareem wa mzikiti wa Namadzi ku Chiradzulu ayankhulapo pa za kuchotsedwa kwa chikwangwani cha Good Samaritan chomwe chinaikidwa pa malo a mzikiti.

Mbusayu Wilson wanena kuti akuluakulu a mpingo wa Good Samaritan komanso akuluakulu omwe amayang’anira mzikitiwu akhala akukumana m’mbuyomu kumakambilana kuti achotse mtandawu.

A Wilson anati zangochitika kuti mtandawo wachotsedwa patangotha masiku ochepa pataonongedwa chikwangwani cha asilamu ku Blantyre.

‘’Tinapempha kuti timange chikwangwani cha mpingo wathu pa malo omwe chagumulidwa paja, sitinamange iwo asakuziwa iyayi, koma kumapeto kwake titamanga patha chaka ndi miyezi, ndi m’mene amatipeza kumatiuza kuti otithandiza athu akuti chinthu chija chichoke komanso chatalika kuposa zina nde muchichose mukachiyike kwina,” anatero a Wilson.

Iwo anaonjezera kunena kuti a ku likulu kwa Good Samaritan anawalimbikitsa kuti akhale pansi ndi asilamu akambilane bwinobwino.

Malingana ndi a Wilson, iwo anakumana ndi a mfumu adelalo ndipo amfumu anadabwa nayo nkhani chifukwa nkhaniyi analinso atayizizilitsa nthawi ina.

“Ndipo patangoyambika za chikwangwani cha ku Blantyre chija, ndipamene m’modzi mwa akulu akulu omwe amayang’anila mzikitiu anabwera kuzatiuza kuti pasanathe masiku awiri tichotse chikwangwani chathu pa mzikitiu.

‘’Zitatelo ife tinapitaso kwa amfumu kukadandaula. Ndipo amfumu anakakamba ndi wa mkulu wa kumzikiti kuja, ndipo amfumuwo anayankhidwa kuti sizingatheke kuti chinthu chija chikhale pano, choncho atatiuza ife, tidakawauzanso a kulikulu, ndipo iwo adati alibe zipangizo zoti timangilenso chipilala china,” anatero a Wilson.

Anaonjezera kunena kut mpingo wawo unawauza Asilamu kut ngati angapereke zipangizo zomangila chikwangwani china, iwo achotsa chikwangwanicho koma Asilamu anatiuza kuti sizingatheke.

“Titawauzanso a kulikulu kwathu anatiuza kuti tiwauze kuti chinthucho achichosepo koma simunali mwa mtendele koma munali mwakusagwilizana chifukwa pa chiyambi panali mgwirizano oti chinthucho chikhalepo lelo lino akutikakamiza kuti tichosepo chikwangwani,’’ anatelo a Wilson.

Poyankhulapo, Sheikh Hussen Abdul Kareem anati iwo sanachotse chikwangwanicho pofuna kubwezera zomwe zinachitika ku Blantyre.

M’modzi mwa omwe amachotsa chikwangwanicho anayankhulanso kuti kuchotsa kwa chikwangwanicho ndi kwa mtendere chifukwa chikwangwanicho chinachotsedwa m’busa wa mpingo wa Good Samaritan ali pompo.

Pakadali pano apolisi azofufuzafuza adakafufuza za nkhaniyi.

One comment on “M’busa, Sheikh ayankhulapo pa kuchotsedwa kwa chikwangwani

  1. As people of god,we should take an example of Jesus Christ,to have peace all the time.Remove the post for the sake of peace please.

Comments are closed.