Fisi anakana nsatsi: A Mutharika ati sakukhudzidwa pankhani ya simenti

Advertisement

Mtsogoleri wakale wadziko lino yemweso ndi mtsogoleri wa chipani chotsutsa boma cha DPP a Peter Mutharika akanitsitsa mwamtu wagalu kuti akukhudzidwa pankhani ya simenti yomwe ilimkamwa mkamwa.

Izi zikutsatira kutchulidwa kwa a Mutharika kuti ndiwo anagula matumba oposa 1 miliyoni a simenti a ndalama zokwana K5 biliyoni koma osapereka msonkho.

Nkhaniyi ikumasonyeza kuti matumba asimentiwa analowa m’dziko muno pogwiritsa ntchito dzina la a Mutharika.

Koma poyankhapo pa nkhaniyi, a Mutharika ati iwo sakudziwa kalikonse pa nkhaniyi ndipo anenetsa kuti iwo sanatume munthu kuti awagulire simenti pa nthawi yomwe anali mtsogoleri wa dziko lino.

Popitilira ndikukanitsitsa, iwo kudzela kwa mlembi wawo Linda Salanjira ati zikuwadabwitsa kuti iwo anakagula bwanji simenti ochuluka chonchi pomwe panthawiyi analibe ndondomeko ili yonse yamamangidwe.

A Mutharika atinso iwo samapanga malonda ogulitsa simenti choncho ati zomwe anthu akunena kuti iwo ndiokhudzidwa pankhaniyi ndibodza lankunkhuniza ndipo ati palibe abale ulionse ndi kampani kapena munthu yemwe anagulitsa simentiyu.

Masiku apitawa apolisi anamanga anthu angapo mokhudzidwa ndi nkhani yi omwe ndikuphatikizapo a Norman Chisale omwe anali mkulu oyang’anira chitetezo pomwe a Mutharika anali pampando wa mtsogoleri wadziko.

Advertisement