Mayi waphedwa ndi afisi ku Ntcheu

Advertisement
Malawi24.com

Mayi wina yemwe anamwa mowa ndi kugona panjira waphedwa ndi afisi, m’mudzi mwa Doviko mfumu yaikulu Mpando ku Ntcheu.

Watsimikiza zankhaniyi ndi mneneri wa apolisi m’bomali a Hastings Chigalu omwe azindikira mayiyu ngati mai Ellenita Zembeleni azaka makumi asanu, mphambu zisanu ndi imodzi (56).

Malingana ndi a Chigalu, mayiyu monga mwachizolowezi loweluka lapitali pa 18 July anapelekeza amunake a Emiliano Kwaderanji a zaka 74 kumalo ena omwera mowa m’dera lomweli.

Ali kumalo omwera mowawa onse anautunga mowawu koma patsikuli bambo Kwaderanji anali oyamba kuimika manja kuti mowawo wawakwana ndipo ananyamuka nthawi yabwino kupita kunyumba kwawo kuwasiya akazawo akumwabe chakumwa choledzeletsacho.

Pomwe nthawi imati 11 koloko usiku, mai Kwaderanji anauyamba ulendo wakunyumba kwawo mopanda mantha komatu paja akulu adati chizolowezi chidaphetsa kunda.

Ulendo ulimkati, mayiyu anatopa kaamba kaukali wachakumwacho kotelo anangoganiza zopeza malo pakathengo kuti abeko tulo pang’ono ndicholinga choti mowa ukakatuka ayambileso ulendo wake, ukalodzedwadi sumanunkha.

Ali mkati mwatulo, fisi m’modzi anamupeza mzimayiyu ndipo mayiyu anakuwa kuti anthu amuthandize ndipo mwamwayi bambo wina yemwe anava fuuwu anathamanga kukamuleletsa mayiyu ndipo anamuthamngitsa fisi uja.

Apa bamboyo anaganiza kuti fisiyo wathawira kutali ndipo anayamba ulendo kuthamangira kumudzi kukaitana anthu ena kuti adzathandizane kumunyamula mzimayi oledzerayo poti yekha sakanawakwanitsa.

Naye bamboyo anakadziwa sanakamusiya yekha mayiyo kaamba koti pomwe amafika ndi anthu ena kuti azamunyamule mayiyu, anapeza ziwalo za mayiyu zili kukamwa kwa afisi ochulukirapo.

Malingana ndi mneneri wa polisiyu, anthuwa anathamangitsa afisiwa ndipo anakwanitsa kupulumutsa ziwalo zochepa za thupi la mayi Kwaderanji.

Mai Ellenita Zembeleni anali ochokera mmudzi mwa Sawu mfumu yaikulu Phambala m’boma lomwelo la Ntcheu.H

Advertisement