Patricia Kaliati ayamikira wapampando wa MEC

Patricia Kaliati

M’modzi mwa akuluakulu a mgwirizano wa Tonse, a Patricia Kaliati, ayamikira wapampando wa bungwe loyendetsa zisankho la MEC a Justice Dr Chifundo Kachale ponena kuti akugwira bwino ntchito.

A Kaliati amayankhula izi mu mchipinda cha College of Medicine ku Blantyre komwe bungwe la MEC likuyendetsera ndondomeko yonse yachisankho chamtsogoleri wadziko chomwe chinachitika lachiwiri pa 23 June.

Poyankhula ndi Malawi24, a Kaliati anati ndiosangalala kwambiri ndi mmene akugwilira ntchito Dr Kachale ponena kuti sakuona kukaikitsa kwina kuli konse ndipo ati izi sizomwe amayembekezera.

Iwo anati malingana ndikuti a Kachale apatsidwa mpandowu munyengo yovuta kwambiri komaso sanapatsidwe nthawi yochuluka yokonzekera, amaona ngati pakhala mavuto adzaoneni zomwe sizili choncho ndipo ati ndiwokondwa.
Mai Kaliyati omwe amadziwika ndi dzina loti a Kweni ati potengera ndimmene akuyendetsera zotsatira zachisankhochi, wapampando wa MEC yu waonetsa kuti ndimunthu otsata malamulo komaso osalolera zachibwana.

“Ifetu tikuona kuti chisankho chikuyenda bwino kwambiri ndipo pakadali pano sitinaone vuto kwenikweni ndipo tikuona Mulungu akukhala kumbali yathu komaso china ndiyamike wapampando wa MEC.

“Wapampando wathu ndi mbambande akugwira ntchito mwaukadaulo wake ndipo zachita kusonyeza kuti anapitadi kusukulu. Mutha kuona kuti akunena kuti sathamanga, akunenaso kuti akufuna kuthana ndi madandaulo onse bwinobwino mosakondera mbali ndipo ife tikuyamika pantchito yabwino yomwe akugwira,” watelo Kaliati.

Iwo anati ndizosakhala kuti wapampandoyu akugwira bwino ntchito ndi atolankhani kuyelekeza ndimomwe zinalili chaka chatha pomwe anati atolankhani ena amachititsidwa manyazi kaamba kofusa mafunso.

A Kweni anati nthawi yafika tsopano yoti anthu awone kusintha pazinthu zosiyanasiyana m’dziko muno pomwe zotsatila zosatsimikizika zikuonetsa kuti mtsogoleri wa mgwirizano wa Tonse a Lazarus Chakwera, akutsogola.

Pakadali pano wapampando wa MEC wati bungweli likhala litamaliza chilichose chachisankhochi pakutha pamaola 36 kapena 48 kuchokera dzulo ndipo apempha anthu kuti apitilire kudekha ndukusunga bata.

Advertisement