Chiwelengero cha opezeka ndi Coronavirus chafika pa 481

Advertisement

Chiwelengero cha anthu omwe apezeka ndikachilombo ka Corona komwe kakumayambitsa matenda a COVID-19 chafika pa anthu 481 tsopano.

Watsimikiza za nkhaniyi ndi Dr John Phuka omwe ndi wapampando wagulu lomwe mtsogoleri wadziko lino a Peter Mutharika anakhazikitsa kuti liziyang’anira ntchito yolimbana ndikufala kwa mliri wa COVID-19 omwe wavuta padziko lonse.

Dr Phuka omwe amayankhula lachinayi anati pakadali pano anthu ena makumi awiri mphambu zisanu ndi imodzi (26) apezekaso ndikachilombo ka Corona m’dziko muno.

Wapampandoyu anati mwa anthu omwe apezekaso ndikachilomboka, asanu ndi anayi 9 ndi ena mwa anthu omwe angofika kumene lachinayilo kudzera pa bwalo la ndege la Kamuzu ku Lilongwe pomwe amachokera mdziko la Kuwait.

Iwo anati kupatula pa anthuwa ochokera mdziko la Kuwait wa, ku Lilongwe ndiku Blantyre kwapezekaso anthu asanu asanu ndipo ati nako ku Salima kwapezeka anthu anayi pamene ma boma a Mzuzu, Thyolo ndi Zomba kose kwapezeka mmodzi mmodzi.

“Mmaola makumi awiri ndi mphambu zinayi (24) apitawa ku Lilongwe kwapezeka anthu asanu ndi anayi mwa asanuwa akuganiziridwa kuti apezeka ndikachiromboka kaamba kogundana ndi anthu omwe alinako kale.

“Ku Blantyre nako kwapezekaso anthu asanu ena ndipo awiri mwa asanuwa ndiogwira ntchito zachipatala pamene mmodzi akuganiziridwa kuti anakhudzana ndi munthu wina yemwe ali kale ndikachoromboka koma awiri enawo tikufufuzabe momwe atengera kachiromboka,” anatelo Dr Phuka.

Mkuluyu anati chosangalatsa mchakuti pakadali pano chiwerengero cha anthu omwe achira kunthendayi chakwera pomwe zadziwika kuti mmaola 24 apitawa anthu ena khumi achira kunthendayi.

A Phuka anati chiwerengelochi chapangitsa kuti chiwerengero cha anthu ochira chifike pa pa 65 ndipo anati chiwerengero cha anthu omwe amwalira ndi nthendayi pakadali pano chinakali pa anayi (4) pomwe paja.

Mwa anthu 481 omwe apezeka ndi nthendayi m’dziko muno, anthu 382 anawapeza ndikachilomboka pomwe amachokera kunja kwa dziko lino ndipo anthu 86 anatenga kachilomboka m’dziko momuno ndipo anthu 13 akufufuzidwabe ngati alindikachiromboka.

A Phuka anatiso madotolo akupitilirabe kuyeza anthu osiyanasiya kuti awone ngati ali ndikachilomboka ndipo analangiza anthu m’dziko muno kuti apitilize kutsatila malangizo omwe unduna wa zaumoyo ukumapeleka pofuna kupewa kutenga kachilomboka.

Advertisement