MEC ipangitsa kawuniwuni wa maina a ovota

Advertisement

Bungwe loyendetsa zisankho m’dziko muno la MEC lapempha anthu omwe analembetsa pa mavoti kuti akatsimikize ngati maina awo ali mu nkaundula ndipo izi zichitika lachitatu ndi lachinayi sabata ino.

Watsimikiza zankhaniyi ndi mneneri wa bungwe la MEC a Sangwani Mwafulirwa omwe ati panthawiyi malo onse adzikhala otsekulu kuyambira nthawi ya 8 koloko mmawa mpaka 4 koloko masana.

A Mwafulirwa ati omweso anasintha malo awo oponyera vote akuyenera apite kumalowa kuti akatsimikize ngati maina awo anasinthidwadi ndicholinga choti asakumane ndizovuta patsiku la chisankho.

Mkuluyu wakumbutsaso anthu omse omwe akhale akupita kumalowa kuti asamaiwale kutenga chiphaso chawo chovotera koma ati panthawiyi sipakhala kupangaso ziphaso zina kwaomwe ziphaso zawo zinatayika.

Apa a Mwafulirwa anati kwaomwe ziphasozi zinatayika kapena kuonongeka asadandaule kaamba koti bungweli layika ndondomeko yoti anthuwa adzaloledwe kukaponya nawobe voti patsiku lachisankho.

Iwo ati anthu omwe sanalembetse pakalambera wa mavote chaka chatha sakuyenera kupita nawo ku malowa ponena kuti malingana ndi gamulo la khothi anthuwa sakuyenera kuzaponya nawo voti.

“Tikufuna tidziwitse mtundu wa a Malawi kuti lachitatu ndi lachinayi lomwe ndipa 10 komaso 11 June, MEC itsekula malo onse m’dziko muno kuti anthu omwe analembetsa mkaundula wa voti akawone ngati mayina awo alipodi mkaundulamo.

“Monkumbutsana, malingana ndichigamulo cha khothi, oyenera kuponya voti ndiokhawo omwe analembetsa pokonzekera chisankho cha chaka chatha choncho omwe analembetsa mkaundula wa posachedwapa akupemphedwa kuti asapite ku ma center ku chifukwa maina awo sakapezeka,” watero Mwafulirwa.

Mneneri wa MEC yu watiso pofuna kuchepetsa kudzadza kwa anthu ku malo omwe kawuniwuniyu akachitikire, bungweli lakhazikitsa njira yowona ngati munthu dzina lake lilipo mumkaundulayu kudzera pamafoni a mmanja.

Iwo ati anthu omwe akufuna kuwona ngati dzina lawo lilipo mu mkaundulayu atha kumayimba pa nambala ya *720# ndikutsatila ndondomeko yonse yomwe idzibweletsedwa pafonipo ndipo ati izi ndizaulele kwa makasitomala a Airtel ndi TNM.

Pakadali pano, tsiku leni leni lomwe chisankhochi chichitike silinadziwikebe koma pali chiyembekezo choti aphungu anyumba ya malamulo akambirana komaso kutchula tsikuli munzokambilana zawo sabata ino.

Masiku 150 omwe bwalo lamilandu linapeleka pa 3 February kwa bungwe la MEC oti likhale litapangitsa chisankho cha mtsogoleri wa dziko akutha pa 2 mwezi wa July.

Advertisement