Mutharika waloza chala zipani zotsutsa kuti ndilo gwero la zipolowe pandale

Advertisement

Mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika adzudzula mchitidwe wa zipolowe pandale omwe wakula m’dziko muno koma ati gwero lazonsezi ndi ndikuyankhula udyo kwa atsogoleri azipani zotsutsa.

A Mutharika amayankhula izi lachisanu kudzera kwa owayankhulira wawo a Mgeme Kalirani potsatira zipolowe zomwe zakhala zikuchitika mdziko muno kuyambira pomwe bungwe la MEC linakhazikitsa nyengo yokopa anthu.

Mtsogoleri wadziko linoyu wati ndiokhumudwa ndizomwe zinachitika kwa Msundwe m’boma la Lilongwe ponena kuti anthu omwe analowa chipani cholamura cha DPP akuchitiridwa nkhanza ndi anthu ena kaamba kachiganizo chawo.

Iwo ati auzidwa kuti anthuwa akuthamangitsidwa mderali kaamba kopanga chisankho chotuluka chipani chotsutsa cha MCP ndikulowa DPP zomwe anenetsa kuti sizabwino kudziko la Malawi lomwe limatsata mfundo za demokalase.

“Ndikufuna ndiwakumbutse a Malawi onse kuti monga ndakhala ndikunenera mmbuyomu, zipolowe pandale sizoloredwa kwa ife ngati dziko lotsata mfundo za demokalase ndipo zikuenera kutsutsidwa kwabasi,” atelo a Mutharika kudzera mwa a Kalirani.

A Mutharika kudzera kwa a Kalirani ati ndiokhumudwaso ndizomwe zachitika lachisanu ku Phalombe komwe galimoto za mtsogoleri wachipani cha UTM a Saulos Chilima zakagendedwa pomwe amakapangitsa msonkhano.

Koma iwo aloza chala azitsogoleri azipani zotsutsa ponena kuti ndiomwe apangitsa zipolowezi kaamba ka malankhulidwe awo onyoza pamisonkhano yawo yomwe akhala akupanga mwezi uno.

“A Mutharika ndiokhumudwaso ndizomwe akupanga azitsogoleri otsutsa boma pomayankhula mawu obweretsa udani pamisonkhano yawo yomwe akhala akupanga posachedwapa.

“Zipolowe pandale zomwe zachitika lachisanu ku Phalombe ndi ku Mulanje zabwera kaamba ka azitsogoleri azipani zotsutsa ndi otsatira awo omwe amasangalala ndi kuchemelera zoipa zomwe zinachitikira otsatila DPP omwe anazuzidwa ku Ndirande pomwe amapelekeza a Mutharika,” atero a Mutharika.

Iwo atsindika kuti kunyozana pandale kuthe ndipo alangiza atsogoleri onse andale kuti asiye kuyankhila zinthu zobweretsa udani komaso ati mkwabwino kuti atsogoleri azipani onse azingonena mfundo zawo osati kutukwanizana pamisonkhano.

A Mutharika alamula apolisi kuti afufuze mofulumira milandu yonse yomwe yachitika yokhudza zipolowe pandale ndipo ati anthu onse omwe amayambitsa izi akuyenera kumangidwa ndikulandira chilango.

Kumayambiliro a mwezi uno, anthu atatu omwe ndi abanja limodzi anamwalira kaamba kazipolowe pandale kutsatira kuotchedwa kwanyumba yomwe amakhala ku Lilongwe yomweso inali ofesi ya chipani cha UTM.

Advertisement

3 Comments

  1. I guess if overcome this election they will set fire sanjika for sure , because I can smell fully misunderstanding in between MCPUTM in future.

  2. Mutalika ndiye vuto la zipolowe alibe umunthu komano wakalamba sangalamulireso a malawi

  3. Zimakhala zodabwitsatu, mdziko la demokalasi, ndipo ndzosasangalatsa, a pulezidenti akunena zomveka, Koma futso nkumati, mdziko lomwelo la demokalasi munthu ngat akugwira ntchito m’boma then akupanga nao zandale, kungokalowa chipani chisutsa (Tonse alliance) mkumawatchotsa ntchito (fire) mkuluyuu wachipani chipani chinachi kaya mmati ndaniso mwamutchosa pompano bcos wakalowa chipani chosutsa Kodi Demokalasi ikugwira ntchito pamenepo….?

    Think twice isakhale demokalasi kwazanu okha komaso kumbukilani mnymba mwanumo kut muli nzotani Zosemphana ndi demokalasi…..

    Mwapha anthu Ku Lilongwe, mudziko lomwelo la demokalasi pepani mngayambe kundililitsa… Mulungu Akuonaneni zikomo

Comments are closed.