Chiwelengero cha opezeka ndi Corona chafika pa 36

Advertisement

Chiwelengero cha anthu omwe apezeka ndi kachilombo ka Corona m’dziko muno chafika pa anthu 36 tsopano.

Izi ndi malingana ndi nduna ya zaumoyo m’dziko muno a Jappie Mhango omwe amayankhula Lolemba ku Lilongwe pa msonkhano wa atolankhani komwe analengeza kuti anthu ena awiri apezekaso ndikachilombo ka Corona.

A Mhango ati m’modzi mwa anthuwa ndi bambo wa zaka 47 yemwe amakhala ku Chileka mumzinda wa Blantyre ndipo ati munthuyu anafika m’dziko muno posachedwapa kuchokera m’dziko la Tanzania komwe matendawa avutaso kwambiri.

Iwo anati munthu winayo ndi bambo wazaka 45 yemwe amakhala ku Area 2 ku Livimbo mu mzinda wa Lilongwe koma ati awa alibe mbiri iliyose yoti anayenda zomwe anati zikusonyeza kuti nthendayi yafalikira mmadera ambiri.

Iwo anati izi zapangitsa chiwerengero cha anthu omwe apezeka ndikachilomboka kufika pa 36 ndipo ati ndizosangalatsa kuti pakadali pano chiwerengero cha anthu omwe amwalira ndi nthendayi chidakali pa atatu pomwe ati ochila adakaliso pa anayi pomwe paja.

“M’maola 24 apitawa malo oyezera matendawa ku Mzuzu anayeza anthu okwana 34 ndipo mmodzi yekha ndiyemwe wapezeka ndi kachilomboka pamene ku Lilongwe anayeza anthu atatu ndipo mmodzi ndiyemwe wapezeka nako.

“Nako ku Blantyre anayeza anthu okwana 24 koma m’modzi ndiyemwe wapezeka ndi kachilombo ka Corona zomwe zapangitsa kuti chiwerengero chifike pa 36 tsopano,” watelo Mhango.

Ndunayi inqtti pakadali pano madotolo atumizidwa kuti akayeze azibale awo a anthuwa ndipo alangiza anthu m’dziko muno kuti apitilize kutsatira malangizo omwe undunawu ukumapeleka pofuna kupewa kutenga kachilomboka.

Ndunayi yati pakadali pano Ku Lilongwe kwapezeka anthu 23 kuphatikiza imfa yamunthu m’modzi pamene ku Blantyre chiwerengelo cha omwe apezeka ndi kachilomboka chafika pa 9 kuphatikizaso imfa yamunthu mmodzi.

Maboma a Chikwawa, Nkhotakota, Karonga komanso Zomba konseku kunapezeka odwala matenda a COVID-19 mmodzi mmodzi.

Advertisement