Anthu asanu apezeka ndi Corona ku Lilongwe

Advertisement

Chiwelengero cha anthu omwe apezeka ndi kachilombo ka Corona komwe kakumayambitsa matenda a Covid-19 m’dziko muno chafika pa anthu makumi awiri ndi mphambu zitatu (23) tsopano, ndipo asanu mwa iwo apezeka ndi kachilombola maola 24 apitawa.

Izi ndimalingana ndi mlembi wamkulu mu unduna wa zaumoyo, Dr. Dan Namarika omwe amayankhula m’mawa wa lachitatu pa msonkhano wa atolankhani mumzinda wa Blantyre.

A Namarika anati m’modzi mwa anthuwa anali m’dziko la India masiku apitawo ndipo akukhala ku Area 3 mumzinda was Lilongwe.

Dr Namalika anati maola 24 apitawa, anthu asanu ndi m’modzi (6) apezeka ndi kachilomboka ku Kaliyeka komaso ku Area 25 onse mumzinda wa Lilongwe zomwe ati ndizodandaulitsa kwambiri.

Iwo anati chikupeleka chiopsezo kwambiri ndichoti omwe apezeka ndinthendayi akuchokera m’madera omwe mumakhala anthu ochuluka zomwe anati zitha kupangitsa kuti chiwelengerochi chikwere kwambiri masiku akubwerawa.

Apa iwo anati unduna wa zaumoyo wayamba kafukufuku pa anthu ena 17 omwe akuwaganizira kuti angakhale kuti ali ndi kachilomboka kaamba koti anakumana/kukhalira limodzi ndi omwe apezeka ndithendawa.

“Pakadali pano kwa maola 24 apitawa dziko lino lapeza anthu asanu ndi mmodzi (6) omwe apezeka ndi nthendayi zomwe zapangitsa chiwerengero cha anthu onse omwe apezeka ndi thendayi kufika pa 23.

“Izi zabweretsa chiopsezo kwambiri kaamba koti nthendayi yapezeka ndi anthu omwe akuchokera mmadera omwe kumakhala anthu ochuluka ngati ku Kaliyeka komaso ku area 25 zomwe zapangitsa kuti tikhale pantchito yofufuze kuti anthuwa anakhudzana ndindani ndipo chiwerengelochi chitha kunka chikukwelabe,” anatero Namarika.

A Namarika anachenjeza kuti nkofunika kuchitapo kanthu msanga pa vutoli chifukwa kupanda kutero, dziko la Malawi silitha kuthana ndi vutoli.

Mkuluyu watinso chokhumudwisa china nchoti pali madalaivala ena amagalimoto onyamula katundu omwe akumakana malangizo azaumoyo pa nkhondo yolimbana ndi mliri wa korona zomwe ati zikuika pachiopsyezo dziko lino pa ntchito yolimbana ndi vutoli.

A Namarika anatiso pali chiopsyezo choti anthu oposela zikwi zisanu (50,000) atha kufa ndi nthendayi mdziko muno pakutha chaka ndipo kafukufuku wawo akuonetsa kuti mzinda wa Lilongwe ndiomwe uli pachiopsyezo kwambiri cha mliliwu ngati satsata njira zopewera nthendayi.

Pakadali pano anthu awiri ndi omwe anamwalira ndi nthendayi mdziko muno masabata apitawo pamene anthu atatu omwe amadwala nthendayi achila.H

Advertisement