Mabungwe adzudzula amayi oyendayenda omwe amazunza ana awo

Advertisement

Amabungwe omenyera ufulu wa ana ati ndi pofunika kuti malamulo agwirepo ntchito pa amayi oyendayenda omwe amatengera makasitomala awo kuchipinda komwe kuli ana.

Bungwe lina lomenyera ufulu wa ana lanena izi poyankhulapo pa zomwe mayi wina wauza Malawi24 kuti mwana wake amazuzika iye akamagwira nthcito yake.

Mayiyu yemwe ndi mmodzi mwa amayi oyenda yenda yemwe tinakumana naye ku malo omwela mowa ku Nancholi mu mzinda wa Blantyre.

Mayiyu yemwe zaka zake ndi zochepela makumi awiri, wati mamuna wake anapita ku dziko la South Africa kukasaka ntchito, iye ali ndi pa thupi pa miyezi isanu ndipo mamuna wakeyo samapeleka chithandizo cha mtundu wina uliwonse.

Iye adakhala movutika mpaka mwana wake anabadwa.

“Mwana atabadwa mavuto anga adachuluka kwambili kuposela mmene ndidali oyembekezera. Chakudya komanso zovala za mwana zimandisowa.

“Ndidayamba kusakasaka ntchito mmakomo mwa wanthu koma sinapezeke.

“Izi zinandipangitsa kuti ndiyambe nchitidwe oyendayenda kuti ndizipeza chakudya changa cha tsiku ndi tsiku komanso mwana wanga, ndizimupatsa chithandizo chokwanira,” mayi oyendayendayi adandaula.

Izi ngakhale zili chonchi, mayiyu akumayika pa chiopsezo moyo wa mwana wake tsiku ndi tsiku pa nthawi yomwe wapita kukasaka ndalama.

Iyeyu wati amayenda mu malo omwera mowa osiyanasiyana mu mzinda wa Blantyre komwe amalipila chipinda chogonamo alendo chomwe chidamangidwa moyandikana ndi malo omwera mowa ndikumadikila kuti kunja kude.

Kukada amatsekela mwana wake muchipindacho iye kupita ku malo omwela mowa kukakopa amuna kuti akagone naye amupatse ndalama.

“Ndipo ndimayendayena malo omwela mowa osiyanasiyana muno mu mzinda wa Blantyre monga ku Bangwe, kwa Manje, kwa Kachere komanso kuno ku Nancholi kuti ndipeze ndalama yoti ndizizithandizila komanso ndizithandiza mwana wanga.

“Ndimakalipila chipinda chogonamo alendo zomwe zinamangidwa kuyandikila malo omwelamo mowa. Kukada ndimamutsekela mwana wanga mu chipindacho kumapita mmalo omwela mowa kumakawakopa amuna kuti ndigone nawo andipatse ndalama.

“Mamunayo akapezeka ndimamutengela ku chipinda chogonamo a lendo chomwe ndalipila chija,” alongosola Mmayi oyendayenda.

Ndipo mayiyu amatengela kuchipindako azibambo osiyanasiyana osawaziwa kuti amapanga chani ku chipinda komwe kuli mwana wake wachichepele uja, zomwe zimayika pa chiopsezo moyo wa mwanayo.

Mkhalidwe umenewu ndiochulukila mu mzinda wa Blantyre pomwe azimayi ena oyendayenda amatengela ana awo mu malo omwela mowa pazifukwa zosiyanasiyana.

Ena mwa amayiwa amatengela ana awo malo omwela mowa kumakagulitsako malonda osiyanasiyana monga mang’ina, fodya, matchesi komanso zina zambili mwana wachichepele ali kumbuyo.

Izi zimapangitsa kuti ana azipuma mpweya omwe wasakanikilana ndi fodya ndi zina zambili zomwe zingathe kuononga miyoyo ya anawo.

Mchitidwe umenewu wadandaulitsa amabungwe. A Godknows Maseko omwe amamenyera ufulu wa ana anati mchitidwe uwu siwabwino poti ukuyika miyoyo ya ana pa chiopsezo.

“Mkhalidwe umenewu siwabwino ndipo malamulo akufunika agwilepo ntchito. Ana samaloledwa kupezeka malo amenewaja mwa njila ina iliyonse.”

“komanso ndikuganiza kuti zomwe ife amabungwe tikuchita sizikukwanila powonetsetsa kuti ufulu wa ana sukuphwanyidwa. Komanso owona za malamulo sakupanga zokwanila poteteza ufulu wa ana.”

“Ndikanakonda kuti owona za malamulo ayendele malo amenewa ndikukamanga azimayi omwe akupanga mchitidwe otelewu. Ngakhale malamulo a ana amanenetsa kuti mwana ayenela kutetezedwa ku chinachilichonse komanso malo omwe angayike pa chiopsezo moyo wa mwana,” anatelo a Maseko.

Bambo Maseko anaonjezelapo kuti akonza misomkhano yofuna kuphunzisa za ufulu wa ana.

Mneneli wa a polisi a James Kadadzera ayankhulapo kuti iwo monga apolisi afufuza ndipo apangangapo kanthu kwa wina aliyense apezeke akupanga mchitidwe otelewu.

“Tipanga kafukufuku ndipo ife a polisi tipanga zoyenelela kwa makolo onse apezeke akuchita mchitidwewu kuti titeteze ana ku malo omwe angawononge miyoyo yawo,” adatelo a Kadadzera.

Mu chaka cha 1989 maiko osiyanasiyana anapanga ubale ndikupanga malamulo oteteza ufulu wa ana monga, ufulu otetezedwa, ufulu ophunzila, ufulu otenga nawo mbali mu zinthu zosiyanasiyana komanso ma ufulu ena ambiri.

 

 

 

Advertisement