Chiwerengero cha anthu opezeka ndi corona chakwera

 

Munthu wina m’boma la Blantyre yemwe wangobwera kumene kuchokera ku United Kingdom wapezeka ndi matenda a Covid-19, zomwe zapangisa kuti akhale muthu wachinayi opezeka ndi thendayi ku Malawi kuno.

Nduna ya za umoyo m’dziko lino, a Jappie Mhango, atsikimiza za khaniyi ndipo anati muthu yemwe wapezeka ndi thendayi adayezedwa lachisanu ku sukulu ya ukachenjede ya college of medicine ku Blantyre.

“Kutengera ndi zotsatira za tsopanozi, titha kusikimiza kut chiwerengero cha anthu omwe apezedwa ndi thendayi chakwera kufikano pa folo (4). Ndipo zizindikiro zake zikufanana ndi anthu omwe apezeka nayo ku Lilongwe,” a Mhango adafotokoza.

Nduna ya za umoyoyi, idachenjeza a Malawi kuti dziko lino tsopano lili pa khondo yolimbana ndi mliriwu choncho nkofunika kuti kugwirana manja.

Iwo anati boma la Malawi lili pakalikiliki kupeza njira zogonjetsera kufala kwa thendayi zomwe zina mwa izo ndi; kuonesetsa kuti anthu onse oganizilidwa ayezedwe.

Kutengera ndi a Mhango, boma lili tcheru kuonesetsa kuti anthu akusatira malangizo monga kusamba m’manja ndi sopo, kusapezeka m’magulu a anthu ochuluka, komaso boma likupereka zipangizo zozitetezera kwa anthu omwe ali pachiwopsezo chotenga thendayi makamaka ogwira ntchito ya za umoyo.

“Unduna wa za umoyo ukuziwa za kuchepa kwa anthu ogwira ntchito ya za umoyo ndichifukwa chake boma lawonjezera ndalama zina kuti anthu ena alembedweso ntchito,” adatero a Mhango.

A Mhango adapitirizaso kunena kuti boma lakonzaso zipangizo zothandizila mpweya wabwino ku zipatala zonse za chigawo cha pakati komaso lawonjezera zipangizo zina zokwana makumi awiri (20) kumalo omwe azithandizilako odwala m’thenda ya COVID-19.

“Zipatala zonse za m’maboma zili ndi malo omwe apatulidwa kuti azithandizilamo omwe apezeke Kapena omwe apezeka ndi m’thendayi. Ndipo m’malo ena monga chigawo cha pakati ndi m’zipata za dziko lino, ntchitoyi yayamba kale,” a Mhango anatero.

Advertisement