Anthu aphwanya ndi kuwononga sikimu ya Ulongwe kamba kobweresa matsoka  

Advertisement

Anthu a m’dera la m’fumu yaikulu Nyambi m’boma la Machinga aphwanya ndi kuwononga zipangizo za sola zomwe zimathandizila ulimi wa nthirira za ndalama yokwana k55 miliyoni, poganizila kuti sikimuyo ikubweresa matsoka komaso minyama m’deralo.

Nyuzipepala yina ya Malawi News Agency (MANA) yati pa 22 marichi chaka chomwe chino, anthu a m’mudziwo adakawononga zipangizozi pa malo ochitira ulimi wa nthirira a Ulongwe, komaso adabapo zipangizo zina monga zida za sola za ndalama yokwana K12 miliyoni, ma pampu  awiri a madzi, ma panelo 16 a sola, ma batile awiri ndi zotchajila ziwiri, ma wilibala 4 (anayi) komaso ma paipi amadzi.

Wachiwiri kwa mneneri wa polisi ya Machinga, a Ngwashape Msume, adati anthuwo adasokhana ndikuzikonzekeresa okha kupita kukawononga pa malo ochitira ulimi wa mthirirawo.

A Msume adatiso anthuwo adawuza a polisi kuti minyama ndi matsoka m’deralo adayamba m’chaka cha 2018, nthawi imene boma lidayamba kumanga sikimu ya Ulongwe kudzela mu pulojeketi ina ya zakusintha kwa nyengo.

“Mayi wina wotchedwa Daina John, ochokera m’mudzi wa a Mapiri, m’fumu yaikulu Nyambi m’boma lomwero la Machinga,  adamwalira ma paipi atamugwera pa chifuwa chake nthawi imene amathandizila kusitsa ma paipiwo m’galimoto,” adatero a Msume.

Iwo adatiso ana ophunzila pa sukulu ya Malundani yomwe yawandikana ndi sikimu ya Ulongwe, akhala akukomokakomoka mosaziwika bwino.

“M’modzi mwa atsikana ena omwe adakomoka, adawuza anthu a m’mudziwo kuti abiti John, omwe adamwalira pa sikimuyo, ndi omwe adamunyamula iye atakomoka,” a Msume adafotokoza.

Izi ndi zomwe zidapangisa anthuwo kukaphwanya komaso kuwononga sikimu ya Ulongwe poganizila kuti matsoka onsewa akubwera kamba ka sikimuyo.

Pakadali pano, apolisi sananjate (kugwira) muthu wina aliyense kamba kakuti akufufuzabe za khaniyi.

Sikimu ya Ulongwe ili pansi pa pulojeketi ya zakusintha kwa nyengo yomwe yagwiridwa m’maboma a Mangochi ndi Machinga kuyambira chaka cha 2015 mpaka 2019, ndipo ntchitoyi idali ya ndalama zoposa US$5 miliyoni.

Advertisement