Mutharika akana kusainira malamulo achisankho, kuchotsa makomishonala a MEC

Advertisement

Mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika akana mwa ntu wagalu kusainira kusintha kwa ena mwa malamulo oyendetsera chisankho m’dziko muno.

Izi zadziwika pomwe a Mutharika kudzera kwa owayankhulira awo a Mgeme Kalirani anapangitsa msonkhano wa atolankhani lachiwiri mu mzinda wa Blantyre.

Nkhaniyi ikutsatira mgwirizano omwe aphungu anyumba ya malamulo anapanga mwezi watha pomwe anagwirizana kuti ena mwa malamulo oyendetsera chisankho m’dziko muno asinthidwe.

Koma poyankhula pa msonkhano wa atolankhaniwu, a Kalirani anati mtsogoleri wa dziko lino waona kuti nkosayenera kuti iye avomereze kuti malamulo ena oyendetsera chisankho m’dziko muno asinthidwe.

A Kalirani anati a Mutharika apanga chiganizo chokanachi kaamba koti akuona kuti kusintha kwina kutha kukhala kuphwanya mfundo zakusalowelelana kwa mphamvu ndi ntchito za nthambi za boma la demokalase.

“Pankhani imeneyi, mtsogoleri wa dziko lino wanena kuti sasayinila malamulo omwe nyumba yamalamulo inakambilana mwezi watha. Pali zifukwa zingapo koma chachikulu nchoti dziko lino limayendetsedwa ndi malamulo akulu.

“Ndiye tikamapanga malamulo alionse timaonetsetsa kuti agwirizane ndizomwe konsitushoni yathu ikunena ndiye a Mutharika awona kuti malamulo omwe nyumba ya malamulo inapanga akusemphana ndizomwe konsitushoni ikunena, ndichifukwa chake akana kusayinila,” anatero a Kalilani poyankhulira a Mutharika.

Mneneri wa mtsogoleri wadzikoyu anatinso a Mutharika akana kuchotsa ntchito akuluakulu a bungwe la MEC kuphatikizapo wapampando wa bungweli mayi Jane Ansah ati chifukwa nyumba ya malamulo sidapereke ndondomeko zomwe bungwe la MEC lidalakwisa.

Iwo anati chodabwitsa komaso choseketsa kwambiri nchoti anthu akuti MEC inalephera kuyendetsa bwino zotsatira za chisankho cha mtsogoleri wadziko chaka chatha pomwe MEC yomweyo ndiyomwe inayendetsa zisankho za makhansala komaso aphungu anyumba ya malamulo.

Apa iwo anati sanapeze vuto lililonse lomwe akuluakulu a MEC anachita ponena kuti ndizosatheka kuti bungweli liyendetse bwino zisankho za makhansala ndi aphungu ndikulephera za mtsogoleri wa dziko.

“A Mutharika atawona pempho la PAC kuti achotse makomishonala a MEC, mtsogoleri wadziko linoyu wapezaposo zinthu zingapo zomwe ziliso zolakwika. Munali zachidule zomweso sizinathandize kwenikweni choncho a Mutharika akanaso kuti iwo sachotsa ntchito ma komishonala a ntchito,” anawonjezera a Kalirani.

A Kalirani anawonjezera kuti a Mutharika akukhulupilira kuti zomwe apangazi ndizomwe malamulo adziko lino amanena ndipo ati ngati anthu ali ndi kudandaula kulikose ndikwabwino kutsata njira yabwino yopelekela madandaulo awo.

Advertisement

2 Comments

  1. Adady woyeeee kkkkk muchizungu timati BIG BRAIN
    KEEP UP MR MUNTHARIKA

  2. Ndipo 100% collect
    2024 popanga zisankho zinazo malamulo amenewo azayambireso pamenepo.

    Mr President nawoso Ali ndi ufulu sizomwe mukupangazo zofuna kumuona kupusa President Never Never Never

    I said Never

Comments are closed.