Mbiri yalembedwa: khothi lilagamula kuti Amalawi akavoteso

Advertisement

…Chimulirenji apeleke mpata kwa Chilima…

Yemwe adabweretsa mwambi oti sim’nazione anachezera kuziona analinga ataona kuti Lolemba pa 3 February ku Malawi zomwe sizinachitikeko mu mbiri yake zizachitika pomwe khothi lidzagamule kuti kuchitikeso chisankho chatsopano.

Pomwe anthu akhala akuyembekeza mwachidwi chigamulo chabwalo lamilandu la malamulo m’dziko muno kwa miyezi pafupifupi isanu ndi inayi, sizam’maluwaso kuti dziko lino likhala ndichisankho chinaso posachedwapa.

Izi zikutsatira chigamulo chomwe ma mulumuzana asanu motsogozedwa ndi a Healy Potani apeleka chomwe chakomela odandaula onse awiri omwe ndi mtsogoleri wa UTM a Saulos Chilima komaso mtsogoleri wa chipani cha MCP a Lazarus Chakwera.

Odandaula awiriwa anakamang’ala kupempha kuti bwalo lamilanduli lilamule kuti chisankho cha mtsogoleri wa dziko chichitikeso kaamba koti sichinayende bwino kwenikweni.

Atsogoleri azipani ziwirizi anauza khothi kuti mtsogoleri wadziko lino anasankhidwa mwachinyengo ponena kuti pachisankhochi bungwe loyendetsa zisankho linalakwitsa zinthu zochuluka kuphatikiza kuwulutsa kuti a Mutharika ndi omwe apambana pachisankhochi.

Koma bungwe loyendetsa zisankho la MEC omwe anali odandaulidwa oyamba pamlanduwu komaso a Mutharika kudzera kwa owayimilira awo akhala akuwuza bwalo la milanduli kuti pachisankhocho panalibe zovuta ngati momwe amanenera a Chilima ndi a Chakwera.

MEC yakhala ikutemetsa nkhwangwa pamwala kuti inaulutsa zotsatira zomwe zinali zolondola ndipo mbali inayi a Mutharika akhalaso akuuza anthu mumisonkhano yawo kuti iwo ndi omwe anapambana pachisankhochi ndipo amati sanabere.

Linda madzi apite ndipomwe udziti ndadala; Lolemba, ndi tsiku lomwe anthu ambiri anapereka chidwi ndi nthawi yawo ku mawailesi osiyanasiyana omwe amaulutsa chigamulo cha bwalo lamilandu chomwe chinatenga pafupifupi maola khumi ndi awiri.

Mwazina, ogamula milandu asanu omwe ndi a; Dingiswayo Madise, Ivy Kamanga, Mike Tembo ndi a Redson Kapindu motsogozedwa ndi a Healy Potani agamula kuti a Mutharika anasankhidwa mosatsata ndondomeko choncho ati anthu akaimeso pamzere kusankha mtsogoleri wa dziko lino.

A Potani anati bungwe la MEC linalakwitsa zinthu zochuluka pandondomeko yake yowonkhetsa zotsatira zachisankhochi ndipo alamula bungweli kuti lichititse chisankho china cha mtsogoleri wa dziko pasanathe masiku 150 yomwe ndi miyezi isanu kuchokera pano.

“Ndizosatheka kukhala ndichisankho chopanda mavuto koma kafukufuku wathu wapeza kuti pazisankho zapitazi, zovutazi zinafalikira madera ochuluka kotelo kuti upangiri wa zotsatira zenizeni zachisankhochi unasokonezedwa kwambiri.

“Chomcho pakuyenera pachitikeso chisankho china pasanathe masiku 150 omwe ndikuphatikiza masiku akumathero kwasabata komaso kuphatikiza masiku atchuthi.” Watelo Potani popeleka chigamulo.

Iwo anatiso malingana ndimalamulo adziko lino, yemwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko pano a Everton Chimulirenji achotsedwapo ndipo a Chilima abwezeretsedwa kukhalaso wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko monga zinalili pasanafike pa 21 May.

Bwaloli lalamulaso kuti bungwe la MEC lipereke ndalama zomwe a Chilima komaso a Chakwera agwiritsa ntchito pa mlanduwu

Advertisement