Chilima apempha bata

Advertisement

Pamene anthu m’dziko muno akudikira mwachidwi chigamulo cha khothi pa mlandu wa za chisankho sabata lamawa, mtsogoleri wachipani cha UTM a Saulos Chilima apempha anthu onse kusunga bata.

A Chilima amayankhula izi lachinayi kulikulu lachipanichi ku Area 10 mu mzinda wa Lilongwe pa msonkhano wa atolankhani.

Iwo ati dziko la Malawi kuyambira kalekale limadziwika bwino ndi mbiri ya bata komaso mtendere ndipo ati ndikufunika kuti mzika za dziko lino zionetsetse kuti mbiri yabwinoyi isaonongeke makamaka pa nthawi imeneyi pomwe bwalo likuyembekezeka kupeleka chigamulo.

Mtsogoleri wa UTM yu watiso monga pfuko limodzi, anthu mdziko muno adutsa ndi kupulumuka ku mavuto osiyanasiyana limodzi monga; njala, nthenda ndi umphawi ndipo ati sikoyenera kuti pakhale kugawanika pano kaamba ka ndale.

A Chilima atiso mzachidziwikire kuti chigamulo chakhothi chidzakomera mbali imodzo koma apempha kwa amene chigamulo sichidzawakomera kuti adzavomereza ndipo ati omwe chidzawakomere azasangalale koma mopatsa ulemu.

“Inde, pamene tikuyembekeza kupeza chilungamo kuchokera ku khoti, ndi udindo wathu tonse kusunga bata ndi mtendere. Nkhondo siimanga mudzi. Ndife amodzi. Kuchokera kumwera, pakati, kumpoto, tonse ndife aMalawi.

“AMalawi anzanga, tisadane kapena kupasula pfuko lathu lokondekali chifukwa chosiyana zipani kapena kusiyana maganizo pa ndale. Ndife anthu okonda mtendere. Tachokera kutali mu umodzi wathu.” Watelo Chilima.

Iwo apemphaso apolisi kugwira bwino ndikukwaniritsa udindo wawo powonetsetsa kuti m’dziko muno mukhale bata ndi mtendere ndipo chitetezo cha anthu ndi katundu mu nyengo imeneyi chikhale chokwanira.

Apa a Chilima apemphaso apolisi kugwiritsa moyenera mphamvu zawo zovomelezeka ndi malamulo a dziko lino mosachitira nkhanza munthu aliyense ndipo adzudzula apolisi omwe amachitira nkhanza anthu kuti izi sizoyenera.

Mkuluyu wadzudzulaso mchitidwe wakuba ndikuononga katundu wa anthu ena pazionetsero zomwe zakhala zikuchitika m’mbuyomu ponena kuti anthu akuyenera kulemekeza ufulu wa anthu ena ngakhale kuti malamulo a dziko lino amaloleza zionetsero.

Apa a Chilima ati pamene anthu akuchita zionetsero, aliyense ali ndi udindo osunga bata ndi mtendere ndinso kulemekeza ufulu, chuma ndi moyo wa anthu ena ndipo ati pakutero dziko lino lidzapitilira kukhala lamtendere.

Pakadali pano pafupifupi atsogoleri onse azipani zikuluzikulu mdziko muno apempha bata pomwe aliyese akudikira mwachidwi chigamulo chakhothi chomwe chipelekedwe lolemba lino ku Lilongwe

Advertisement