Mayi amangidwa chifukwa chowotcha milomo, m’khosi mwa mwana wake

Advertisement

A polisi ku Mulanje akusunga mayi Loveness Fabiano m’chitokosi chifukwa chowotcha milomo ya mwana wa zaka zisanu pomuganizila kuti anaba nsomba ya Mlamba mu mphika.

Osatira wa mneneli wa a polisi ku Mulanje a Blessings Gama avomeleza kuti mayi Loveness amangidwa ndipo akusungidwa mu chitokosi.

“Tinamvetsedwa kuti Lachinayi sabata yatha, mayi Fabiano anaphika nsomba ndikuchokapo kumusiya mwana ali yekha pakhomo, ndipo pobwerera anapeza kuti milamba yomwe anaphika sikukwanila mumpoto. Izi zinakwiyitsa mayiyu ndipo anatenga chikuni chamoto ndikuotcha milomo, mkhosi komaso pachidale pamwanayu kenako mayiyu anachoka pakhomopo.

“Mnyamatayu analila mosalekeza ndipo achemwali awo a mayi Fabiano atamva kulila mosalekeza analunjikila kukhomoko ndipo anapeza mwana ali ndi matuza amoto mthupi. Kenako achemwali awo a mayi Fabiano anathamangila ndi mwanayu kuchipatala chachikulu cha Mulanje kumene anagonekedwa,” anatero a Gama.

M’mawa wa lachisanu mayi amwanayu analondola mwanayu kuchipatala ndipo apolisi atamvetsedwa za mkhaniyi anapita kukakwizinga mayiyu.

Mayiyu adakasungidwa mchitokosi podikila kuti akaonekele ku bwalo la milandu pamene a polisi akufufuza zina ndi zina.

Mayi Fabiano amachokela mmuzi wa Makuluni, T/A Njema m’bomamo.

Apolisi akulangiza makolo ndi onse omwe amayang’anila kuti azipewa kuchitila an nkhaza za mtundu wina ulionse.

 

 

 

Advertisement