Joseph Nkasa aikila kumbuyo kupambana kwa Mutharika

Advertisement
Joseph Nkasa

….Pomwe Charles Nsaku wati ‘vuto ndiutsogoleri okakamilawu’….

Mphangala ziwiri pamaimbidwe m’dziko muno Joseph Nkasa komaso Chris Charles Nsaku, zaimba nyimbo zotsutsana pa momwe zikuyendera ndale komaso zinthu zina mdziko muno.

Akamuna awiriwa atsutsana pamomwe zinthu zikukhalira kuchokera pomwe dziko lino linali ndi chisankho chapatatu mwezi wa May chaka chatha.

Wayamba zonse ndi Joseph Nkasa yemwe posachedwapa watulutsa nyimbo yomwe ikugwirizana ndikupambana kwa mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika pazisankho zapitazo.

Munyimbo yake yomwe yautsa mapili pachigwayi, Nkasa yemwe amadziwika ndidzina loti Phungu wa amphawi, wati sakuona zachilendo kuti zipani zotsutsa zikudandaula kuti zinabeledwa ponena kuti mawu oti ‘mwatibera’ amasonyeza kulira kwa oluza.

Munyimboyi Nkasa wadzudzula mchitidwe owononga katundu pazionetsero zomwe zakhala zikuchitika potsatira zotsatila za chisankho zomwe wati ndizobwezeretsa chitukuko chadziko lino.

“Chisankho chinapita, oluza analuza, owina anawina. Mpikisano ulionse pamakhala munthu mmodzi owina. Mawu oti mwatibera sangalephere poti kumakhala kulira. Olira satsekedwa pakwamwa popeza misonzi ndi ya ulere. Chomwe chikukhumudzitsa ayamba kuononga zitukuko zawo zomwe.” atero mbali ina ya nyimbo ya Nkasa.

Kolasi yanyimboyi, Nkasa akumafusa kuti; “Muonongeranji zitukuko zanu zomwe? Sukulu zanu zomwe mwaotcheranji? Zipatala zanu zomwe mwaotcheranji? Misewu yanu yomwe mwakumbilanji? Mijigo yanu yomwe mwazuliranji?”

Oyimbayu, munyimbo yomweyi ngakhale sanatchule dzina, wadzudzula bungwe lomenyera ofulu wa anthu la HRDC ponena kuti likumatsogolera anthu kupita kumisewu kukaba ndikukaononga zinthu ena.

“Bungwe lina lomenyera ma ufulu a anthu lalowa uchigawenga. Likumemeza anthu azipita munsewu kuononga katundu, kuphwanya ma sitolo, kuba katundu yense, anthuwa ndi zigawenga. Kuotcha nyumba za anthu, office za police zipatala, sukulu. You are the terrorist, you are the murderer, you are the monster.” watelo Nkasa munyimboyi.

Kumbali inayi, Charles Nsaku yemwe anati ziii pakatipa osatulutsa nyimbo, naye watulutsa nyimbo yodzudzula zipolowe komaso kusagwilizana komwe kulipo pakati pa anthu mdziko muno potsatira chisankho chapitacho.

Koma Nsaku mosiyana ndi Phungu Nkasa, wati zonse zachipolowe zomwe zikuchitika m’dziko munozi ndi kaamba koti munthu wina akukakamila kukhala mtsogoleri wa dziko lino pomwe sizinaenera kutelo.

“Vuto utsogoleri okakamilawu, wabweretsa nkhondo kumalawi padziko ponse. Vuto utsogoleri okakamilawu, wabweretsa nkhawa ku Malawi ndi dziko lonse. Mademo atsiku ndi tsiku, kuononga katundu wa anthu, vuto utsogoleri okakamilawu,” watelo Nsaku mu nyimbo.

Munyimboyi, Nsaku wati pano mzosadabwitsa kuti anthu ambiri m’dziko muno akuthawa ndikumapita ku dziko la South Africa ponena kuti zambiri sizili bwino ku Malawi kuno monga ngati kale kaamba kautsogoleri womwe wati ndi okakamila

Advertisement

2 Comments

  1. Malawi the is big broblem what left now is the war president is fucken sheet we not coming back on that country am taking my family out from the

  2. Charles nsaku is saying the truth,most african leaders doesn’t want to get out once elected as president.Why can’t we take example of other countries in europe or america.It is very rare you see the president saying i am not standing for presidency again.It was only Nelson Mandela who who ruled one term and then step down although people wanted him to continue.
    Most african leaders are like that we were born with a black heart ( selfishness).

Comments are closed.