Ogwira ntchito pakalembera wa umzika apanga m’bindikiro

Advertisement

Anthu omwe anagwira ntchito pa kalembera wa chiphaso cha umzika mchaka cha 2017, ati apanga m’bindikilo sabata yamawa pofuna kukakamiza akuluakulu a bungwe la UNDP komaso boma kuwapatsa ndalama zawo zina.

Izi ndimalingana ndi wachiwiri kwa mneneri wa anthuwa a Philip Masingati omwe ati m’bindikilowu ukuembekezeka kuyamba lolemba pa 16 December kumaofesi a bungwe la UNDP mumzinda wa Lilongwe.

A Masingati ati poyamba anthu omwe anagwira ntchito pakalemberayu analonjezedwa kuti apatsidwa zinthu zambiri zomwe mwa zina anati ndikupatsidwa thandizo lakuchipatala komaso kupatsidwa ndalama ya mayunitsi oimbira lamya koma ati zonsezi sizinachitike.

Iwo ati boma kudzera mwa a Grace Obama Chiumia omwe anali nduna mchakachi, linalamula kuti lionjezera ndalama yamalipiro a anthuwa kuchoka pa K10,000 kufika pa K20,000 patsiku zomwe ati sizinachitike ndipo mmalo mwake anthuwa amapatsidwa K7000 patsiku.

Anthuwa ati anali okhumudwa ndi zomwe zimachitikazi ndipo mmbuyomu akhala akuyesetsa kukumana kuti akambilane ndi akuluakulu a bungwe la UNDP komaso boma koma ati izi sizimaphula kanthu.

A Masingati anati anthu ena omwe anagwira ntchito yakalemberayi atakumana chaka chatha mumzinda wa Mzuzu komwe amakambilana zoyenera kuchita, anamangidwa ndi apolisi ndipo anati akuganiza kuti uku kunali kufuna kuwatseka pakamwa.

“Nthawi imene tinapita kumpoto mu mzinda wa Mzuzu zinapezeka kuti apolisi anatimanga ndipo anzathu omwe anamangidwawo anatha sabata imodzi ali mchitokosi. Atatuluka tinakasuma ku bwalo lamilandu ndipo mlanduwu tinauwina koma boma linakanabe kuti silingatipatse ndalamazo.

“Ifeyo tinafikila bungwe la UNDP pankhaniyi ndipo linaonetsa chidwi choti litipatsa ndalamazo mwezi wa April chaka chino koma mpaka pano bungweli likungothawathawa ndipo mchifukwa chake tikupanga m’bindikilowu omwe uyambe lolemba pa 16 December mpaka pomwe mavuto athu ayankhidwepo,” Watelo Masingati.

A Masingati adzudzulaso mtsogoleri wadziko lino, Peter Mutharika, kaamba koti wakhala akunena kuti amafuna achinyamata mdziko muno adzipita patsogolo koma akulephera kuwathandiza pankhaniyi kuti anthuwa alandile ndalama zawo zotsalazo.

Podziwa kuti akulu ndi mdambo mozimira moto, mkuluyu anati a Mutharika ali ndiulamuliro othetsa nkhaniyi ndikuonetsetsa kuti anthu onse omwe anagwira ntchitoyi alandira ndalama zawo.

Anthuwa apemphaso mabungwe omenyera ufulu wa anthu kuti alowelerepo pa khaniyi kuti chilungamo chidziwike ndikutiso anthu omwe anapanga kalemberayu alandile ndalama zawo zotsalazi.

Advertisement