Sitinaotche nyumba ya Mtambo – DPP

Advertisement
Dausi

Chipani cholamula cha Democratic Progressive (DPP) chatsutsa mwa ntu wagalu zoti otsatira chipanichi ndi omwe awotcha nyumba ya mkulu wa bungwe lomenyera ufulu la HRDC a Timothy Mtambo.

Nyumba ya a Mtambo komaso galimoto yawo zawotchedwa m’bandakucha la chinayi pomwe anthu omwe sakudziwika anaponya bomba la mafuta agalimoto a petulo.

Kutsatira kupsa kwa nyumba komaso galimoto ya a Mtambo anthu ochuluka akuloza chala chipani cholamula cha DPP kuti otsatira ake ndi omwe apanga chipongwechi potsatira zomwe a Mtambo akuchita pomaitanitsa zionetsero.

A Mtambo akumapangitsa zionetsero zokakamiza mkulu wa bungwe la MEC a Jane Ansah kutula pansi udindo wawo ponena kuti analephera kuyendetsa bwino zotsatila za chisankho chapitachi.

Anthu ochuluka m’masamba a intaneti ati akuganiza kuti otsatira a DPP apanga dala izi ndicholinga choopseza a Mtambo kuti asiye kupangitsa zionetsero koma chipanichi chakanitsitsa kuti sichinapange chipongwechi.

Mneneri wa chipanichi a Nicholas Dausi ati chipani chawo sichimapanga zinthu zamtopola komaso zoopsa ngati zimenezi ndipo atsindika kuti omwe apanga chipongwechi si achipani cha DPP.

A Dausi anati Mulungu anawapatsa boma ndiye sizingatheke kuti akhale pansi ndikuyambaso kuwotcha nyumba za anthu awo omwe komaso ati anthu akulakwa kuloza chala chipani chawo pankhaniyi.

“DPP siingapange zimenezo chifukwa Mulungu wabwino anatipatsa boma nde zingathekeso kuti tiyambe kuwotcha nyumba za anthu athu omwe? Mwachidule tingonena kuti ife sitikudziwapo kanthu zankhaniyi komaso ndikutsindika kuti apanga izi si a DPP.

“Ndikutilakwira kutiloza chala ifeyo chifukwa nkhaniyi ndi mlandu wawukulu komaso oopsa nde bwanji tiwasiyile anzathu apolisi kuti ayifufuze bwino bwino nkhaniyi, Kama ayi ndithu DPP siingapange zauchifwambazi,” anatero  a Dausi.

Pakadali pano apolisi kudzera mwa mneneri wawo a James Kadadzera atsindika kuti ayesetsa kugwira komanso kutengera kubwalo la milandu anthu omwe apanga chipongwechi ndipo anthu asadele nkhawa ndinkhaniyi.

Advertisement

One Comment

  1. OK, if its not you then whom do you think? remember that you are tasting your know Medicine

Comments are closed.