Taimitsa kaye zionetsero – Mtambo

Advertisement

Wapampando wa bungwe lomenyera ufulu wa anthu la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) a Timothy Mtambo, alengeza kuti ayamba aimitsa kaye zionetsero pofuna kupereka mpata ku bwalo la milandu lomwe layamba kumva nkhani yokhudza zotsatira za chisankho.

Mulandu wa zotsatila za chisankho cha pa May 21 zomwe a zipani zotsutsa akuti sizinayende bwino, lachinayi wabweleraso mukhothi patapita masiku angapo bwalo la milandu litayimitsa kaye mlanduwu.

Kuyambilaso kumvedwa kwa mulanduwu kwapangitsa kuti bungwe la HRDC kudzera mwa wapampando wake a Mtambo, alengeze zakuimitsidwa kwa zionetserozi.

A Mtambo ati kuimitsidwaku kwadza ndicholinga choti apelekee mpata kuti bwalo la milandu limve bwino bwino mlanduwu komaso kuti iwowo akwanitse kuwutsatira bwino mlanduwu ponena kuti nkhaniyi ikufunika kuika chidwi kwambiri.

Iwo anatiso apanga izi mdicholinga chofunaso kuti mbali zokhudzidwa pa mlanduwu zikwanitse kuwutsatila mlanduwu komaso ati sakufuna kuti omwe akupanga zionetsero anenedwe kuti ndiwo akusokoneza zinthu m’dziko muno komaso mlanduwu.

Mkuluyu wati ngakhale izi zili chonchi, sizikutanthauza kuti iwo ndi gulu lawo asiya kupangitsa zionetsero ndipo ati posachedwa akhala akubweraso ngati wapampando wa MEC a Jane Ansa angakhale asanatulebe udindo wawo.

Omenyera ufuluyu anatiso panthawi yomwe ayimitsa zionetseroyi, bungwe lawo komaso ma bungwe ena omenyera ufulu sikuti angokhala chete koma ati akhala ali kalikiliki kupanga njira zina zokakamiza mai Ansah kutula pansi udindo wawo.

“Zatelemu tikhala tikupanga njira zina imodzi ndi imodzi. Pamene tikuona zamulandu Ku Lilongwe, tikhala tikuganizila kuti tingapange chiyani pofuna kukakamiza boma komaso Jane Ansah kutula pansi udindo koma mosasokoneza kamvedwe ka mlanduwu ku khothi,”anatero Mtambo.

Mlandu wa zotsatira za chisankhowu ukuyenera kukhala utatha pakutha pamasiku 24 kuchokera lachinayi pa 8 August limene ndi tsiku lomwe mlanduwu wayamba kumenyedwa.

Advertisement

One Comment

  1. Thank you for writing in chichewa. This is progress…. Musasiye musatope. ChiTumbukanso ndi ChiYao ndi zilankhulo zina zibwelenso.

Comments are closed.