Apolisi ndi omwe anayambitsa zipolowe – Timothy Mtambo

…apolisi abweze katundu yemwe wawonongedwa….

Wapampando wa bungwe lomenyera ufulu wa anthu la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) a Timothy Mtambo aloza chala apolisi kuti ndiwo akumayambitsa zipolowe pazionetsero zomwe zikuchitika.

A Mtambo amayankhula izi kwa atolankhani lachiwiri pakutha pa zionetsero patsikuli mu mzinda wa Lilongwe zomwe sizinakhale zabata monga momwe a Mtambo akhala akulonjezera m’mbuyomu.

Pazionetserozi galimoto ya apolisi komaso nyumba za apolisi zaotchedwa ndi anthu olusa omwe amapanga nawo zionetserozi ndipo katundu wa nkhani nkhani waonongedwa ndikubedwa m’madera ambiri.

Koma pakuyankhapo pa zazipolowe zomwe zinali mu mzindawu, a Mtambo omwe akutsogolera ziwonetselozi ati gwero la zipolowezi ndi apolisi ponena kuti akumawayamba dala anthu kuti apange zipolowezi.

A Mtambo ati apolisi wa anachita kutumidwa ndiboma kuti asokoneze zionetserezi ndipo ati akudziwa kuti cholinga cha apolisi ndikuti zionetserozi zisachitike zomwe ati sizitheka pokhapokha wapampando wa MEC a Jane Ansa atule pansi udindo.

“Pulani ya apolisi tikuidziwa, pulani yawo inali yoti asokoneze zionetserozi ndicholinga choti a Malawi asayende ndipo anayamba kuthira utsi okhetsa misozi aMalawi osalakwa, zomwe zikutanthauza kuti amafuna kuti kukhale zipolowe kuti apeze mpata kuti aombere anthu.

“Ife tiyenda Malawi yose ndikusainila kuti a Peter Mutharika ndi apolisi akuyenera kulipira a Malawi powazuza miyezi iwiri yonseyi, kuwathira utsi okhetsa misozi anthu osalakwa komaso kuombera anthu osalakwa.” Watero Mtambo.

Iwo atsindika kuti apitilizabe kumaitanitsa zionetsero mpaka mkulu wa MEC a Ansah atatula pansi udindo ponena kuti sanayendetse bwino zisankho za pa 21 May Chaka chino ndipo anenetsa kuti saopa ngakhale akumalandira mauthenga oopsezedwa kaamba kotsogolera zionetserozi.

Advertisement

2 Comments

  1. Iwe chi mutambo you must be very stupit pamodzi ndi ma president ako. You are busy destroying this country.one day you will pay for it. Shame on you ww mu mambwe Weeee. Chindere cjalufikapo. Mwina ndiwe mfiti
    . tutakumwivwisya. Ewwwe. E mtambooo pls know god today.. Ww know there is a country that is founding you to destroy our own country.

Comments are closed.