Anthu omwe akusangalala ndi imfa ya Ngolongoliwa alibe mzeru – Mulli

Advertisement

Mkulu wagulu lachikhalidwe la Mulhakho wa Alhomwe m’dziko muno a Leston Mulli ati ndiokhumudwa kuti anthu ena akusangalala ndi imfa ya mfumu ya a Ngolongoliwa.

Izi zikutsatira zomwe anthu ena pa masamba a mchezo pa intaneti akumalemba zosonyeza kuti anthuwo akusangalala ndi imfa ya mfumuyi.

Koma poyankhula pa msonkhano wa atolankhani mu mzinda wa Blantyre dzulo, a Mulli omwe ndi mkulu wa gulu la Mulhakho wa Alhomwe anati ndimzovetsa chisoni kuti munthu angamasangalale pamene dziko lino lataya m’modzi mwa anthu ofunika kwambiri.

Iwo anati izi ndichisonyezo chotti anthu mdziko muno ataya chikhalidwe ndipo anthu ambiri umunthu wachoka chifukwa munthu wamzeru sangasekelele pamene pamudzi pagwa zovuta ngati momwe zachitikiramu.

Mulli anapempha Mulungu kuti akhululukire onse omwe akupanga izi ndipo analangiza anthu omwe akusekelerawa kut akuyenera kudziwa kuti aliyese amene ali ndi moyo adzalawa imfa.

“Pa chilankhulo chachi alebiki pali mawu oti kalikose kali ndimoyo kadzalawa imfa zivute zitani, kaya lero kaya mawa kaya liti ndipo ngakhaleso anthu amene akumalembawo ndikumanyoza, iwowo abale awo sanamwalirepo? Iwowo sanaonepo maliro?

“Munawona kuti munthu waubongo ogwira bwinobwino akunyoza maliro? Kuzampeza munthu akunyoza maliro mudziwe kuti ameneyo ndi munthu osokonekera maganizo, osazindikira ndiposo ndiopusa chifukwa imfa siimazolowereka. Asiye zimemezo komaso Mulungu awakhululukire chifukwa sakudziwa zomwe akuchita.” anateroMulli.

Mkuluyu anaonjezera kunena kuti malemu Ngolongoliwa anali mfumu ya dziko lonse ndipo amalimbikitsa mtendere komaso analibe tsankho zomwe ati zikuwayenereza kulandira ulemu osati munthu akhale pansi mkumasangalala kuti mfumuyi yatisiya.

Mfumu Ngolongoliwa amwalira lamulungu pa 28 July kaamba kanthenda ya khansa ndipo aikidwa m’manda lero.

Advertisement

2 Comments

  1. Muli himself is wrong by saying that the country has lost the very important person. Every life matters and should treated equal.Its because of that mindset with these politians which sparks the public to make such comments when its the death of politicaly connected people.The public is angly with goverment is spending alot of puplic money on these chief while the public is languishing in poverty with no basic services.

    My question up to date is why are the chiefs ejoying taxi payers money?

  2. Zikomo Mr. Milli chifukwa chaumunthu wanu kuwafunirabe kukhululukiridwa pamaso pa mulungu kusatengera zifooko zawo.
    Madala anga aang’ono anandiuza kuti palibe mphawi maliro kotero wina akaonekeredwa zovuta kumathamangirakoooooo kukamutonthoza

Comments are closed.