Apolisi atsindika kuti zionetsero zisachitikeso m’dziko muno

Mkulu wa a polisi m’dziko muno a Rodney Jose atsindika kuti akuluakulu omwe akutsogolera kupanga zionetsero zokakamiza mkulu wa bungwe la Malawi Electoral Commission a Jane Ansah kutula pansi udindo, asiye kupangitsa zionetserozo.

A Jose amayankhula izi ku likulu la apolisi mdziko muno mu mzinda wa Lilongwe pa msonkhano wa atolankhani komwe amakafotokoza tsatane tsatane wa chikalata chomwe anatulutsa sabata latha chomwe anauza akuluakulu omwe akupangitsa zionetsero kuti asiye.

Pamsonkhano wa olemba nkhaniwu a Jose anati iwo alamula kuti zionetserozi zithe kaamba koti sizabataso ngati momwe omwe akutsogolera zionetserozi a Timothy Mtambo akhala akunenera.

Mkulu wa apolisoyu anati ndizokhumudwitsa kuti katundu wa nkhaninkhani yemweso ndiwa ndalama zochuluka akupitilira kuonongedwa pa zionetsero zomwe a Mtambo analengeza kuti zizichitika la chiwiri komaso lachinayi lililonse mpaka a Ansah atatula pansi udindo.

Iwo anati akudziwa kuti ndiufulu wa anthu kupanga zionetsero monga momwe malamulo a dziko lino amanenera koma sangalore kuti bata ndi mtendere zipitilire kusokonekera mdziko muno.

“Ndikutsimikizireni kuti ngati mkulu wa apolisi mdziko muno ndikudziwa bwino kwambiri zimene lamulo lalikulu limanena pankhani yokhudza ufulu omwe a Malawi onse ali nawo kuti akumane ndikupanga zionetsero.

“Akhala akunena kuti zionetserozi ndizabata ndi mtendere koma ndikufuna ndifuse anthu kuti kodi zionetserozi ndi zabatadi ngati momwe akhala akunenera? Zionetserozi zapangitsa kuti katundu awonongeke nde pachifukwa chimenecho tikuona kuti mkwabwino kuti zionetserozi zither,” anatero Jose.

Mkuluyu anapitiliza kunena kuti sangalore kuti zionetserozi ziyambeso kuchitika tsiku ndi tsiku monga momwe mabungwe omwe akutsogolera akhala akunenera ponena kuti izi zingapangitse kuti dziko lino likhale lopanda mtendere komaso lilowe chisawawa.

Pamsonkhano wa atolankhaniwu panaliso mkulu wa asilikali mdziko muno a Vincent Nundwe omwe anati asilikali apitiliza kupeleka chitetezo mogwirizana ndi apolisiwa popeleka chitetezo ndicholinga choti bata libwerere msanga.

Akuluakulu awiriwa aantsindikaso kuti iwo samagwira ntchito zawo mokondera chipani chili chose ndipo anatsutsa zoti iwo akumafuna kusangalatsa chipani cholamula cha DPP.

Advertisement

2 Comments

  1. Zipolopolo basi osanyengerela ife sitidya ndale ngati anauza ife zisatikhudze zisankho zinatha pa 21may

Comments are closed.