A Muluzi asusula chilonda

Advertisement

Ochita ziwonesero ndikusakondwa kwa zotsatira za chisankho cha pa 21 May, awonetsa mkwiyo wawo kwa mtsogoleri wakale wa dziko la Malawi a Bakili Muluzi powakumbutsa za mlandu wawo wakatangale.

Padziwonetsero zomwe zidachitika lachinayi m’dziko muno, ochita ziwoneselowa adatenga ma uthenga wowakumbutsa a Muluzi pa zamulandu wakatangale wokwana K1.7 billion womwe ukadali ku bwalo la milandu.

Mauthenga ena, omwe ochita ziwoneselowa anatenga ndiwowadzudzula a Muluzi kuti asalese kuchita ziwonetsero zokakamiza mkulu wa bungwe loyendesa chinsakho la Malawi Electoral Commission (MEC) mayi Jane Ansa kutulula pansi udindo.

Kumayambiriro a sabatayi, a Muluzi adayitanitsa atsogoleri a mabungwe omwe akukonza ziwonetsero zokakamiza mayi Ansah kutula pansi udindo kunyumba kwao komwe mwazina amawapempha atsogoleri wa kusiya kuchita ziwonetsero m’dziko muno kwasabata imodzi.

A Muluzi akuwaganizira kuti anasakaza ndalama za boma pomwe iwo anali mtsogoleri wa dziko lino m’zaka zapakati pa 1994 kufikila 2004.

Mlandu wa katangale wa a Muluzi, watha zaka zoposa zisanu ukadali ku bwalo lamilandu, ndikutsatira kusapeza bwino kwa mtsogoleriyu yemwe wakhala akupita kuzipatala za m’mayiko ena kukalandila thandizo la makhwala.

Advertisement