Tulani pansi udindo – MLS yauza a Ansah

Advertisement

Bungwe la Malawi Law Society lapempha mkulu wa bungwe la zisankho m’dziko muno a Jane Ansah kuti atule pansi udindo.

Izi ndimalingana ndichikalata chomwe bungweli latulutsa lachinayi chomwe watikitira ndi mlembi wa gululi a Martha Kaukonde.

Mumchikalatachi, bungwe la oyimilira anthu pamilanduli lati ndizomvetsa chisoni kuti kuchokera pomwe bungwe loyendetsa zisankholi linalengeza kuti pulezidenti Peter Mutharika ndiwo anapambana, m’dziko muno mulibe bata komaso mtendere.

Iwo ati ngakhale kuti palibe lamulo lomwe likukakamiza wapampando wa MEC kutula pansi udindo, kunali kwabwino kuti a Jane Ansah alingalire bwino zaudindo wawo.

Bungweli lati mai Ansah akuyenera kuganizira bwino kaamba koti mpungwepungwe omwe ulipo m’dziko muno ndi chifukwa choti anthu anthu ambiri sakukondwa kuwaona iwo akugwira ntchito ngati wapampando wabungweli.

“Bungwe la Law Society likupempha wapampando wa bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) kuti mozama aganizire ndikuunikira ubwino okhala mu ofesi pomwe kukhala kwakwe mu ofesimo kukuoneka kuti ndikomwe kwabweretsa chisokonezo m’dziko muno ndi chipwilikiti pa ndale,” latero bungwe la oyimilira anthu pamilandu.

Bungweli latiso ngakhale kuti anthu ali ndi ufulu opanga zionetsero ngati momwe anthu akupangira pokakamiza mai Ansah kutula pansi udindo, omwe akutsogolera komaso kupanga nawo zionetserozi akuyenera kuganizira kuti nkhaniyi ili kubwalo lamilandu.

Malawi Law Society yati ikudziwa kuti anthu ali ndiufulu koma lati sibwino kumapanga zionetsero pamene nkhaniyi ili ku khothi ndipo ati chodandaulitsaso chachikulu ndichoti zionetserozi sizikumakhala zabata.

Bungweli lapemphaso mtsogoleri wadziko lino kuti otsatira chipani chawo asiye kuletsa anthu kupanga zionetsero ndiposo ati chisiye kupanga misonkhano yosangalala kuti anapambana zisankho pomwe nkhaniyi ili ku khothi.
Chikalatachi chapemphaso azitsogoleri a zipani za MCP ndi UTM kuti asiye kukambapo nkhani yazisankho yomwe ili kubwalo lamilandu akamapanga misonkhano, ponena kuti uku ndikuphwanya malamulo.

Malawi Law Society yapemphaso atsogoleri azipani onse omwe akukhudzidwa ndi nkhaniyi kuti akhale pansi ndikukambirana kuti athetse kusamvana lomwe kulipo ndicholinga choti zinthu ziyambebkuyenda bwino ngati kale.

“Malingana ndi malamulo adziko lino, ndiudindo wa a Malawi onse kuonetsetsa kuti dziko lino limangidwe pa umodzi, chilungamo, ulemu komaso mtendere kuti litukuke ndikupita patsogolo ndipo bungwe lathu liyang’anitsitsa ndi chidwi chochitika chili chonse pa nthawi ino,” chikalatacho chatero.

Chikalatachi chatumizidwa kwa wapampando wa bungwe la MEC a Jane Ansa, a Lazarus Chakwera a MCP, Saulos Chilima a UTM, mkulu wa apolisi a Rodney Jose, Sipikala wa nyumba ya malamulo a Catherine Hara, wapampando wa bungwe lomenyera ufulu la HRDC a Timothy Mtambo komaso kwa mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika.

Advertisement

One Comment

  1. Sizikuveka mkomwe nde munthu amatula pasi udindo nkhani ili kukhothi ? Nde chilungamo palibe kwa inu kulibwino kungosiya kuyankhula inu moti simukudziwa kuti zosezi zikuchitika chifukwa cha ndale?nanga tipex yemweyo akadawina chilima kapena chakwera bwezi kuliso philosophy? amalawi vomerezani kut ndale ndi nkhondo komaso mudziwe tanthauzo la ndale . musiyeni wowina anawina kale ife tikufuna zitukuko osati Dpp,kapena MCP kapena utm.ife tikufuna mtsogoleri wa umunthu osat kut pot ndine mnyamata kapena m’busa ayi , m’busa wabwino sasowa pakamwa kapena nkhope.musiyeni professor agwire ntchito ife tayamika kale kulandira zitukuko

Comments are closed.