Mamuna apha chibwenzi atakanizidwa kukwatilana

Advertisement
Police

Mamuna wina wa zaka 49 m’boma la Rumphi ali m’manja mwa apolisi ataombera ndikupheratu chibwenzi chake kaamba koti makolo a awiriwa amawakaniza kuti asakwatilane chifukwa ndi pachibale.

Watsimikiza zankhaniyi ndi mneneri wa apolisi m’boma la Rumphi a Henry Munjere omwe anati izi zidachitika lamulungu mdera lotchedwa Kanyenjere m’bomali.

A Munjere ati oganizilidwawa ndi a Sandrey Zgambo yemwe anapha bwezi lake Queen Luhanga, 40,  yemwe panthawiyi anali akuchokera ku kumapemphero ku Nthalire.

Apolisi ati awiriwa akhala paubwenzi kwa kanthawi ndipo amapanga madongosolo oti posachedwa pompa apangitse ukwati koma zinadziwika kuti awiriwa ndi pa chiblae ndipo makolo awo anakanitsitsa mwantu wagalu kuti akwatirane.

Izi sizinakondweretse a Zgambo komaso bwezi lawo Queen.

Bambo Zgambo anayamba kuganizira zanjira yomwe angathananilane ndi zomwe amakumana nazozi ndipo anapanga chiganizo choti angopha bwenzi lawolo.

Atapanga chiganizochi, mamunayu anapanga njira yoti apeze mfuti yoti achitile chipongwe bwezi lawolo ndipo anaipezadi koma apolisi ati akufufuzabe kuti adziwe komwe mkuluyu anapeza mfutiyi.

Mkuluyu anaombera bwezi lakero pachifuwa la Mulungu lapitali ndipo anthu achisoni anatengera mkaziyu kuchipatala cha Hewe komwe madotolo anauza anthuwa kuti mai Luhanga wo anali atafa kale.

Apolisi anatengera a Zgambo ku likulu la apolisi m’bomali komwe akusungidwabe pomwe akuyembekeza kukaonekera kubwalo lamilandu ndi kuyankha mulandu wakupha munthu.

Pakadali pano apolisiwa achenjeza kuti anthu asiye mchitidwewu ndipo ati m’malo mwake anthu adzikhala pansi ndikukambirana ndipo ati zikakanika kukambitsana pachiweniweni azitengera nkhaniyi ku polisi osati kupanga chiganizo chakupha.

Advertisement