A Mutharika akhalira chithumba – atero a Jeffrey

Advertisement

Mlembi wamkulu wa chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) a Grezelder Jeffrey wati mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika ndi amene wakhalira chithumba cha chitukuko.

Poyankhula ku Dedza pamene a Mutharika amatsekulira damu la Bwanje, a Jeffrey anauza a Malawi kuti ino si nthawi ya ndale koma ya chitukuko chomwe ku Malawi kuno opereka wake ndi a Mutharika.

“Palibeso kumene angakupatseni chitukuko, wopereka chitukuko m’dziko lino la Malawi ndi Professor Peter Mutharika,” anatero a Jeffrey.

A Jeffrey anapitiriza kunena kuti a Mutharika amapereka chitukuko mofanana ku Malawi konse kuno ndipo anathokoza anthu a ku Dedza poyamikira zitukuko zomwe a Mutharika apereka mu ulamuliro wawo.

Iwo anauza anthu a ku Dedza kuti damu lomwe lamangidwa ndi la iwowo kuti apindule.

Poyankhula zokhudzana ndi zisankho za pa May 21, a Jeffrey anati owina anapezeka ndipo amabungwe anagwirizana nazo zotsatira zomwe anatulutsa a Malawi Electoral Commission.

M’mawu awo, a Mutharika anati achita chitukuko mu dziko lonse la Malawi mosatengera kuti ndi komwe anawasankha kapena ayi.

“Ngakhale simunandivotere kuno ku Dedza ndibweretsa chitukuko kuno,” a Mutharika anatero.

Mtsogoleri wa dziko linoyu anapempha a Malawi kuti agwire naye ntchito limodzi kuti dziko lino litukuke.

Advertisement

One Comment

Comments are closed.