Zisankho zinayenda bwino, sindikutula pansi udindo – Jane Ansah

Advertisement

Wapampando wabungwe loyendetsa zisankho m’dziko muno la Malawi Electoral Commission (MEC) a Jane Ansah ati chisankho chapitachi chinayenda bwino ndipo sakuona chifukwa choti iwo atulire pansi udindo wawo.

Mai Ansah amayankhula izi Lolemba pomwe amacheza ndi imodzi mwa nyumba zoulutsira mawu m’dziko muno komweso ndikuyankhula kwawo koyamba chichitikileni chisankho chapatatu mwezi watha pa 21.

Izi zikutsatila zomwe amabungwe omenyera ufulu komaso zipani zotsutsa za Malawi Congress Party (MCP) United Transformation Movement (UTM) akufuna kuti a Ansah atule pansi udindo wawo.

Mabungwe ndi zipanizi zikufuna kuti mai Ansah atule pansi udindowu kaamba kolephera kuyendetsa bwino zotsatila za zisankho zapitazi ponena kuti chipani cholamura cha Democratic Progressive (DPP) chinabela.

Koma poyankha pazomwe zipanizi ndi mabungwewa akhala akunena, wapampando wa MEC yu wati zisankhozi zinayenda bwino kwambiri ndipo ati ndichitsanzo cha zisankho zomwe zayendetsedwa bwino kuno Ku Africa.

Iwo anatsindika kuti palibe yemwe anabela zisankhozi ponena kuti malingana ndi ndondomeko yomwe bungwe lawo linaika, palibe yemwe anakatha kukwanitsa kubela zisankhozi mwanjira iliyonse.

“Malingana ndi ndondomeko yazisankho yomwe tinaika, ife timkagwira ntchito ndi anthu komaso mabungwe osiyanasiyana komaso oyimilira zipani zonse omwe amayang’anira momwe zinthu zikuendera mmalo mose momwe mumachitikila zachisankhochi.

“Ife ndiokhulupilira kuti zisankhozi sizinabeledwe komano sitingakambe zambiri potengera kuti nkhaniyi ili kubwalo la milandu nde tiyeni tidikire paja malamulo sakutilora kukamba zankhani yomwe ili mukhothi.” anatero Ansah.

Wapampandoyu ananenanso kuti bungwe lawo linayankha madandaulo onse omwe analandira okhudza chisankhochi zomwe zikutsutsana ndi zomwe chipani cha MCP chakhala chikunena kuti mavuto awo ena sanaunikilidwe.

Pankhani yokhudza zionetsero zomwe zikuchitika kuwakakamiza kuti atule pansi udindo wawo, mai Ansah ati pakadali pano sangatule udindo wawo ponena kuti iwo sakuona chomwe analakwitsa kamba koti anagwira ntchito yawo molingana ndi malamulo adziko lino.

Iwo akuti adikira kuti nkhaniyi igamulidwe kaye ndipo akhothi akagamula ndipomwe adzaone ngati mkoyenera kutula pansi udindowo kapena ayi ndipo adzudzula amabungwe komaso azipani omwe akuchita zionetsero kuti iwo atule pansi udindo.

Mai Ansah anati izi zikuonetsa kuti anthuwa sakudziwa chomwe akuchita ponena kuti chanzeru chomwe anthuwa anapanga ndikutengera nkhaniyi ku bwalo lamilandu koma ati zipanizi ndi mabungwewa akuyenera kudikila kaye chigamulo cha khothi kusiyana ndikupanga zionetsero.

“Ine ndimalemekeza malamulo. Iwo akulemba izi koma a Saulos Chilima apita Ku khothi kutanthauza kuti akufuna khothi ligamule kuti zinthu sizinayende bwino ndiye iwowo akuyenera adikire bwalo lakhothili. Asatenge malamulo mmanja mwawo. Asiyeni akhothi ayendetse nkhaniyi mundondomeko yake.

“Mulanduwu uli kukhothi choncho sindingakambe zambiri komano ndikumadabwa kuti omwe akuti nditule pansi udindowo, omwewo akhala ofufuza omwewo ogamula milandu? ndidikira chigamulo chakhothi ndipomwe ndizapange chiganizo ndikadzava kuti khothi lagamula kuti chiyani.” a Ansah anatero.

Mai Ansah anatsutsaso mwa mtu wagalu nkhani zomwe zakhala zikuveka kuti iwo anauza ogwira ntchito ku MEC kuti adzakhala okondwa ngati a Mutharika atapambana chisankho chapitachi komaso ati zomwe anthu akumatumizilana zoti iwo agwidwa ndi ndalama zambiri mdziko la South Africa, ndi bodza la mthelatu.

Pakadali pano mabungwe omwe amachititsa zionetsero zokakamiza kuti a Ansah atule pansi udindo ati apitilizabe kuchita zionetserozi kufikila zomwe akufuna zitatheka.

Advertisement

One Comment

  1. If u did bribe chair indeed u killing future leaders of tomorrow inu mwakalamba kale mngowonongamo ndi opani mulungu akakulangani ndi pls judges our living God must help u to come together with truth and your trutb will build our nation . Mec chair killing our nation.

Comments are closed.